Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Ndimvereni Mulungu pomwe ndikunena madandawulo anga; tetezani moyo wanga ku chiopsezo cha mdani. |
| 2 |
| Ndibiseni ku chiwembu cha anthu oyipa, ku gulu laphokoso la anthu ochita zoyipa. |
| 3 |
| Iwo amanola malilime awo ngati malupanga, amaponya mawu awo olasa ngati mivi. |
| 4 |
| Iwo amaponya mivi yawo ali pa malo wobisala kwa munthu wosalakwa; amamulasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha. |
| 5 |
| Iwo amalimbikitsana wina ndi mnzake pa chikonzero chawo choyipa, amayankhula zobisa misampha yawo; ndipo amati, “Adzayiona ndani?” |
| 6 |
| Iwo amakonzekera zosalungama ndipo amati, “Takonza ndondomeko yabwino kwambiri!” Ndithu maganizo ndi mtima wa munthu ndi zachinyengo. |
| 7 |
| Koma Mulungu adzawalasa ndi mivi; mwadzidzidzi adzakanthidwa. |
| 8 |
| Iye adzatembenuza milomo yawoyo kuwatsutsa ndi kuwasandutsa bwinja; onse amene adzawaona adzagwedeza mitu yawo mowanyoza. |
| 9 |
| Anthu onse adzachita mantha; adzalengeza ntchito za Mulungu ndi kulingalira mozama zomwe Iye wazichita. |
| 10 |
| Lolani wolungama akondwere mwa Yehova ndi kubisala mwa Iye, owongoka mtima onse atamande Iye! |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/064.mp3
150
64