Buku Loyera
|
| 1 |
| Imvani mau anga, Inu Mulungu, pamene ndikukudandaulirani. Tetezani moyo wanga kwa mdani woopsa. |
| 2 |
| Tchinjirizeni ku upo wachiwembu wa anthu oipa, tetezeni ku chiwawa cha anthu ochita zoipa. |
| 3 |
| Iwo amanola lilime lao ngati lupanga, amaponya mau obaya ngati mivi. |
| 4 |
| Amabisalira anthu osalakwa namaŵalasa modzidzimutsa ndi mopanda mantha. |
| 5 |
| Amalimbikira za chiwembu chao, amakambirana zoti atche misampha yobisika, amanena kuti, “Angatiwone ndani?” |
| 6 |
| Amaganizira zoipa nkumati, “Takonza mochenjera ndithu chiwembu chathu.” Malingaliro ndi zofuna za mtima wa munthu nzobisika. |
| 7 |
| Koma Mulungu adzaŵaponya mivi. Motero mwadzidzidzi iwo adzalasidwa. |
| 8 |
| Adzaŵaononga chifukwa cha zokamba zao, onse oŵapenya adzapukusa mitu. |
| 9 |
| Pompo anthu onse adzachita mantha, adzasimba zimene Mulungu wachita, adzalingalira zomwe Mulungu wachitazo. |
| 10 |
| Chauta adalitse anthu ake mtendere ndi chimwemwe zikhale nao, anthu akondwere chifukwa cha Chauta |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/064.mp3
150
64