Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo. Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni; kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa. |
| 2 |
| Inu amene mumamva pemphero, kwa inu anthu onse adzafika. |
| 3 |
| Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo, Inu munakhululukira mphulupulu zathu. |
| 4 |
| Odala iwo amene inu muwasankha ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu! Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu, za mʼNyumba yanu yoyera. |
| 5 |
| Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri, |
| 6 |
| amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu, mutadziveka nokha ndi mphamvu. |
| 7 |
| Amene munakhalitsa bata nyanja kukokoma kwa mafunde ake, ndi phokoso la anthu a mitundu ina. |
| 8 |
| Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu; kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera. Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe. |
| 9 |
| Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira; Inuyo mumalilemeretsa kwambiri. Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi kuti upereke tirigu kwa anthu, pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi. |
| 10 |
| Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake, mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake. |
| 11 |
| Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka, ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka. |
| 12 |
| Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira; mapiri avekedwa ndi chisangalalo. |
| 13 |
| Madambo akutidwa ndi zoweta ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu; izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/065.mp3
150
65