Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Pfuulirani kwa Mulungu, dziko lonse lapansi. |
| 2 |
| Yimbirani ulemerero wa dzina lace; Pomlemekeza mumcitire ulemerero. |
| 3 |
| Nenani kwa Mulungu, Ha, nchito zanu nzoopsa nanga! Cifukwa ca mphamvu yanu yaikuru adani anu adzagonjera Inu, |
| 4 |
| Dziko lonse lapansi lidzakugwadirani, Ndipo lidzakuyimbirani; Adzayimbira dzina lanu. |
| 5 |
| Idzani, muone nchito za Mulungu; Zocitira Iye ana a anthu nzoopsa. |
| 6 |
| Anasanduliza nyanja ikhale mtunda: Anaoloka mtsinje coponda pansi: Apo tinakondwera mwa Iye. |
| 7 |
| Acita ufumu mwa mphamvu yace kosatha; Maso ace ayang'anira amitundu; Opikisana ndi Iye asadzikuze. |
| 8 |
| Lemekezani Mulungu wathu, mitundu ya anthu inu, Ndipo mumveketse liu la cilemekezo cace: |
| 9 |
| Iye amene asunga moyo wathu tingafe, Osalola phazi lathu literereke. |
| 10 |
| Pakati munatiyesera, Mulungu: Munatiyenga monga ayenga siliya. |
| 11 |
| Munapita nafe kuukonde; Munatisenza cothodwetsa pamsana pathu. |
| 12 |
| Munapititsa anthu oberekeka pamwamba pamitu pathu; Tinapyola moto ndi madzi; Koma munatifikitsa potitsitsimutsa. |
| 13 |
| Ndidzalowa m'nyumba yanu ndi nsembe zopsereza, Ndidzakucitirani zowinda zanga, |
| 14 |
| Zimene inazichula milomo yanga, Ndinazinena pakamwa panga pasautsika ine. |
| 15 |
| Ndidzakufukizirani nsembe zapsereza zonona, Pamodzi ndi cofukiza ca mphongo za nkhosa; Ndidzakonza ng'ombe pamodzi ndi mbuzi. |
| 16 |
| Idzani, imvani, inu nonse akuopa Mulungu, Ndipo ndidzafotokozera zonse anazicitira moyo wanga, |
| 17 |
| Ndinampfuulira Iye pakamwa panga, Ndipo ndinamkuza ndi lilime langa, |
| 18 |
| Ndikadasekera zopanda pace m'mtima mwanga, Ambuye sakadamvera: |
| 19 |
| Koma Mulungu anamvadi; Anamvera mau a pemphero langa, |
| 20 |
| Wolemekezeka Mulungu, Amene sanandipatutsira ine pemphero langa, kapena cifundo cace. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/066.mp3
150
66