|
| 1 |
|
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo. Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi! |
|
| 2 |
|
| Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero. |
|
| 3 |
|
| Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu! Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu. |
|
| 4 |
|
| Dziko lonse lapansi limaweramira inu; limayimba matamando kwa Inu; limayimba matamando pa dzina lanu.” Sela. |
|
| 5 |
|
| Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita, ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu. |
|
| 6 |
|
| Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma, iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi. Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye. |
|
| 7 |
|
| Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya, maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina. Anthu owukira asadzitukumule. |
|
| 8 |
|
| Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu, mulole kuti mawu a matamando ake amveke; |
|
| 9 |
|
| Iye watchinjiriza miyoyo yathu ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke. |
|
| 10 |
|
| Pakuti Inu Mulungu munatiyesa; munatiyenga ngati siliva. |
|
| 11 |
|
| Inu mwatilowetsa mʼndende ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu. |
|
| 12 |
|
| Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu; ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi, koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka. |
|
| 13 |
|
| Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza ndi kukwaniritsa malumbiro anga. |
|
| 14 |
|
| Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto. |
|
| 15 |
|
| Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu ndi chopereka cha nkhosa zazimuna; ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi. Sela |
|
| 16 |
|
| Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu. Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira. |
|
| 17 |
|
| Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga, matamando ake anali pa lilime panga. |
|
| 18 |
|
| Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga Ambuye sakanamvera; |
|
| 19 |
|
| koma ndithu Mulungu wamvetsera ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga. |
|
| 20 |
|
| Matamando akhale kwa Mulungu amene sanakane pemphero langa kapena kuletsa chikondi chake pa ine! |
|
|
|
|