Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo. Yehova atikomere mtima ndi kutidalitsa, achititse kuti nkhope yake itiwalire. |
| 2 |
| Kuti njira zanu zidziwike pa dziko lapansi, chipulumutso chanu pakati pa mitundu yonse. |
| 3 |
| Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. |
| 4 |
| Mitundu yonse ya anthu isangalale ndi kuyimba mwachimwemwe, pakuti inu mumaweruza mitundu ya anthu mwachilungamo ndi kutsogolera mitundu ya anthu a dziko lapansi. |
| 5 |
| Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu; mitundu yonse ya anthu ikutamandeni. |
| 6 |
| Nthaka yabereka zokolola zake; tidalitseni Mulungu wathu. |
| 7 |
| Mulungu atidalitse kuti pamenepo malekezero onse a dziko lapansi apembedze Iyeyo. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/067.mp3
150
67