×

Buku Loyera

MASALIMO 67

1
Inu Mulungu mutikomere mtima ndi kutidalitsa, mutiwunikire ndi chikondi chanu,
2
Njira yanu idziŵike pa dziko lonse lapansi, chipulumutso chanu chidziŵike pakati pa mitundu yonse.
3
Mitundu ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
4
Mitundu ya anthu isangalale ndi kuimba ndi chimwemwe, chifukwa Inu mumaweruza anthu mwachilungamo, ndi kuŵatsogolera pa dziko lapansi.
5
Mitundu yonse ya anthu ikutamandeni Inu Mulungu, mitundu yonse ya anthu ikuyamikeni.
6
Nthaka yabereka zipatso zake, Mulungu, Mulungu wathu watidalitsa.
7
Inde, Mulungu watidalitsa, anthu onse a ku mathero a dziko lapansi apembedze Iye.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba