Buku Loyera
|
| 1 |
| Mulungu adzambatuke, adani ake amwazikane. Onse amene amamuda, athaŵe pamaso pake. |
| 2 |
| Amwazeni iwowo monga m'mene mphepo imachitira utsi. Anthu oipa aonongeke pamaso pa Mulungu, monga m'mene sera amasungunukira pa moto. |
| 3 |
| Koma anthu anu Mulungu, akondwere, asangalale pamaso panu, inde, asekere ndi chimwemwe. |
| 4 |
| Muimbireni Mulungu, imbani nyimbo zotamanda dzina lake. Kwezani nyimbo yotamanda Iye amene amayenda pa mitambo. Dzina lake ndi Chauta, musangalale pamaso pake. |
| 5 |
| Atate a ana amasiye ndiponso mtetezi wa azimai amasiye, ndi Mulungu amene amakhala m'malo ake oyera. |
| 6 |
| Anthu osiyidwa, Mulungu amaŵapatsa malo okhalamo, am'ndende amaŵatulutsa kuti akhale pa ufulu, koma anthu oukira, amaŵapirikitsira ku nthaka yoguga. |
| 7 |
| Inu Mulungu, pamene munkatsogolera anthu anu, pamene munkayenda m'chipululu muja, |
| 8 |
| dziko lidagwedezeka, mlengalenga udagwetsa mvula chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu. Phiri la Sinai lidagwedezeka chifukwa cha kubwera kwanu, Inu Mulungu, Mulungu wa Israele. |
| 9 |
| Inu Mulungu, mudagwetsa mvula yokwanira pa dziko. Mudalimbitsanso dziko, choloŵa cha anthu anu, pamene lidaali lofooka. |
| 10 |
| Anthu anu adapezamo malo okhala. Inu Mulungu, mudapatsa anthu osauka zosoŵa zao mwa ubwino wanu. |
| 11 |
| Ambuye apereka lamulo. Nchachikulu chiŵerengero cha amene abwera ndi uthenga wakuti, |
| 12 |
| “Mafumu a magulu a ankhondo akuthaŵa, indedi akuthaŵa. Tsono azimai ku mudzi akugaŵana zofunkha, ngakhale atsalira pakati pa makola ankhosa. |
| 13 |
| “Zofunkhazo zikuwoneka ngati mapiko a nkhunda okutidwa ndi siliva, nthenga zake nzokutidwa ndi golide wonyezemira.” |
| 14 |
| Pamene Mphambe adabalalitsa mafumu kumeneko, ku Zalimoni kudagwa chisanu choopsa. |
| 15 |
| Iwe phiri la Basani, phiri laulemerero, Iwe phiri la Basani, phiri la nsonga zambiri! |
| 16 |
| Iwe phiri la nsonga zambiriwe, chifukwa chiyani ukuliyang'ana mwansanje phiri limene Mulungu adasankha kuti azikhalapo? Ndithu Chauta adzakhalapo mpaka muyaya. |
| 17 |
| Ambuye adafika ku malo ao oyera kuchokera ku Sinai, ali ndi magaleta amphamvu zikwi zambirimbiri. |
| 18 |
| Inu mudakwera kumwamba, mutatenga am'ndende ambiri, ndipo mudalandira mphatso kwa anthu, ngakhale kwa anthu oukira, kuti mudzakhale kumeneko, Inu Chauta Mulungu. |
| 19 |
| Atamandike Ambuye, Mulungu Mpulumutsi wathu, amene amanyamula katundu wathu tsiku ndi tsiku. |
| 20 |
| Mulungu wathu ndi Mulungu wotilanditsa, ndi Mulungu, Ambuye amene amatipulumutsa ku imfa. |
| 21 |
| Koma Mulungu adzatswanya mitu ya adani ake, mitu ya anthu onse oyenda m'machimo ao. |
| 22 |
| Ambuye adati, “Ndidzaŵabweza adani anu kuchokera ku Basani, ndidzaŵabweza kuchokera ku nyanja yozama, |
| 23 |
| kuti musambe mapazi anu m'magazi, kuti agalu anu anyambiteko magazi a adaniwo.” |
| 24 |
| Inu Mulungu, mdipiti wa anthu anu oyenda mwaulemu ukuwoneka, mdipiti wolemekeza Mulungu wanga, Mfumu yanga, wokaloŵa m'malo opatulika. |
| 25 |
| Oimba nyimbo zapakamwa atatsogola, oimba ndi zipangizo ali pambuyo, anamwali oimba ting'oma ali pakati. |
| 26 |
| “Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu. Tamandani Chauta, inu zidzukulu za Israele.” |
| 27 |
| Patsogolo pao pali Benjamini mng'ono wa onsewo, akalonga a Yuda ali pambuyo, ndiponso akalonga a Zebuloni ndi akalonga a Nafutali. |
| 28 |
| Kungani mphamvu zanu, Inu Mulungu, onetsani mphamvu zanu, Inu Mulungu, amene mumatichitira zamphamvu. |
| 29 |
| Chifukwa cha Nyumba yanu ya ku Yerusalemu, mafumu amabwera ndi mphatso kwa Inu. |
| 30 |
| Dzudzulani zilombo zija zokhala m'mabango, ndiponso gulu la nkhunzi lija ndi malikonyani, ndiye kuti akalonga ndi anthu ao. Ponderezani amene amalakalaka ndalama moipa. Abalalitseni anthu okonda nkhondo. |
| 31 |
| Akazembe adzabwera kuchokera ku Ejipito. A ku Etiopiya adzafulumira kugonjera Mulungu pokweza manja ao kwa Iye. |
| 32 |
| Imbirani Mulungu nyimbo, inu maufumu a pa dziko lapansi. Imbani nyimbo zotamanda Ambuye, |
| 33 |
| Chauta amene amayenda mu mlengalenga, mlengalenga wakalekale. Imvani liwu lake, liwu lake lamphamvu zedi. |
| 34 |
| Vomerezani kuti Mulungu ndi wamphamvu, ulamuliro wake uli pa Israele, mphamvu zake zili mu mlengalenga. |
| 35 |
| Mulungu ndi woopsa m'malo ake opatulika, Mulungu wa Israele ndiye amapatsa mphamvu ndi kuŵalimbikitsa anthu ake. Mulungu atamandike. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/068.mp3
150
68