Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Fulumirani kundipulumutsa, Mulungu; Fulumirani kundithandiza, Yehova. |
| 2 |
| Acite manyazi, nadodome Amene afuna moyo wanga: Abwezedwe m'mbuyo, napepulidwe. Amene akonda kundicitira coipa, |
| 3 |
| Abwerere, kukhale mphotho ya manyazi ao Amene akuti, Hede, hede. |
| 4 |
| Asekerere nakondwerere mwa Inu onse akufuna Inu; Nanene kosalekeza iwo akukonda cipulumutso canu, Abuke Mulungu. |
| 5 |
| Koma ine ndine wozunzika ndi waumphawi; Mundifulumirire, Mulungu: Inu ndinu mthandizi wanga ndi mpulumutsi wanga; Musacedwe, Yehova. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/070.mp3
150
70