|
| 1 |
|
| Salimo la Solomoni. Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo, Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu. |
|
| 2 |
|
| Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo, anthu anu ozunzika mosakondera. |
|
| 3 |
|
| Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu, timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo. |
|
| 4 |
|
| Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu ndi kupulumutsa ana a anthu osowa; adzaphwanya ozunza anzawo. |
|
| 5 |
|
| Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse, nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala. |
|
| 6 |
|
| Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa ngati mivumbi yothirira dziko lapansi. |
|
| 7 |
|
| Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika; chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala. |
|
| 8 |
|
| Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi. |
|
| 9 |
|
| Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake ndipo adani ake adzanyambita fumbi. |
|
| 10 |
|
| Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali adzabweretsa mitulo kwa iye, mafumu a ku Seba ndi Seba adzapereka mphatso kwa iyeyo. |
|
| 11 |
|
| Mafumu onse adzamuweramira ndipo mitundu yonse idzamutumikira. |
|
| 12 |
|
| Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira, wozunzika amene alibe wina womuthandiza. |
|
| 13 |
|
| Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa ndi kupulumutsa osowa ku imfa. |
|
| 14 |
|
| Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake. |
|
| 15 |
|
| Iye akhale ndi moyo wautali; golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye. Anthu amupempherere nthawi zonse ndi kumudalitsa tsiku lonse. |
|
| 16 |
|
| Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse; pamwamba pa mapiri pakhale tirigu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni; zichuluke ngati udzu wakuthengo |
|
| 17 |
|
| Dzina lake likhazikike kwamuyaya, lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa. Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye ndipo iwo adzamutcha iye wodala. |
|
| 18 |
|
| Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa. |
|
| 19 |
|
| Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake. Ameni ndi Ameni. |
|
| 20 |
|
| Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese. |
|
|
|
|