|
| 1 |
|
| Inu Mulungu, patsaniko mfumu nzeru zoweruzira, patsaniko mwana wa mfumu mtima wokonda chilungamo. |
|
| 2 |
|
| Motero mfumuyo idzaweruza anthu anu molungama ndiponso anthu anu osauka mosakondera. |
|
| 3 |
|
| Mapiri adzabweretsa madalitso kwa anthu, magomo adzadzetsa mphotho ya chilungamo. |
|
| 4 |
|
| Mfumu idzateteza anthu osauka, idzapulumutsa anthu osoŵa, koma idzaononga anthu ozunza anzao. |
|
| 5 |
|
| Idzakhala moyo pa mibadwo yonse, nthaŵi zonse pamene dzuŵa ndi mwezi zikuŵala mu mlengalenga. |
|
| 6 |
|
| Idzakhala madalitso ngati mvula yogwa pa minda ngati mvula yowaza pa nthaka! |
|
| 7 |
|
| Pa masiku ake chilungamo chidzakula, mtendere udzachuluka, mpaka mwezi utaleka kuŵala! |
|
| 8 |
|
| Idzakhala ikulamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina, kuchokeranso ku Mtsinje mpaka ku mathero a dziko. |
|
| 9 |
|
| Amaliwongo akuchipululu adzaiŵeramira, adani ake adzadya fumbi. |
|
| 10 |
|
| Mafumu a ku Tarisisi ndi akuzilumba adzaipatsa mitulo, mafumu a ku Sheba ndi a ku Seba adzabwera ndi mphatso. |
|
| 11 |
|
| Mafumu onse adzaigwadira ndipo mitundu yonse ya anthu idzaitumikira. |
|
| 12 |
|
| Ndithu iyo idzalanditsa anthu osoŵa amene amaiitana, idzapulumutsa anthu osauka ndiponso opanda woŵathandiza. |
|
| 13 |
|
| Idzamvera chisoni anthu ofooka ndi osoŵa, ndipo idzapulumutsa moyo wa anthu aumphaŵi. |
|
| 14 |
|
| Idzaombola moyo wao kwa anthu oŵapsinja ndi kwa oŵachita zankhanza, pakuti magazi ao ndi amtengowapatali pamaso pake. |
|
| 15 |
|
| Ikhale ndi moyo wautali! Golide wa ku Sheba apatsidwe kwa mfumuyo. Anthu aipempherere nthaŵi zonse, aipemphere madalitso kosalekeza. |
|
| 16 |
|
| M'dziko mukhale chakudya chambiri, pamwambanso pa mapiri pakhale dzinthu. Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni, anthu ake achuluke m'mizindamo ngati udzu wakuthengo. |
|
| 17 |
|
| Dzina lake lisaiŵalike konse, mbiri yake ikhalepobe monga momwe limakhalira dzuŵa. Anthu alandire madalitso chifukwa cha iyo, a mitundu yonse aitche yodala. |
|
| 18 |
|
| Atamandike Chauta, Mulungu wa Israele. Iye yekha ndiye amene amachita zinthu zodabwitsa. |
|
| 19 |
|
| Dzina lake laulemerero litamandike mpaka muyaya. Ulemerero wake udzaze dziko lonse lapansi. Inde momwemo. Inde momwemo. |
|
| 20 |
|
| Ano ndiwo mathero a mapemphero a Davide, mwana wa Yese. |
|
|
|
|