×

Buku Loyera

MASALIMO 73

1
Zoonadi, Mulungu ndi wabwino kwa olungama, kwa anthu oyera mtima.
2
Koma ine ndinali pafupi kuphunthwa, mapazi anga anali pafupi kuterereka.
3
Pakuti ndinkachita nsanje ndi anthu odzikuza, pamene ndidaona anthu oipa akulemera.
4
Iwowo samva kupweteka konse. Matupi ao ndi onenepa ndi athanzi.
5
Saona mavuto monga anthu ena, sazunzika ngati anzao.
6
Nchifukwa chake amavala kunyada ngati mkanda wam'khosi. Amavala nkhanza ngati malaya.
7
Maso ao ndi otupa ndi kunenepa. Mitima yao ndi yodzaza ndi maganizo ofuna kuchita zoipa.
8
Amanyodola ndi kumalankhula zoipa, amadzikuza ndi kumaopseza ena kuti, “Tikupsinjani.”
9
Pakamwa pao pamalankhula monyoza Mulungu kumwamba, ndipo lilime lao ndi losamangika pa dziko lapansi.
10
Nchifukwa chake ngakhale anthu a Mulungu amabwera kwa iwo, ndipo amakhuta zonena zao ngati madzi akumwa.
11
Amati, “Kodi Mulungu angadziŵe bwanji? Kodi Wopambanazonseyo angadziŵe kanthu kalikonse?”
12
Onani, umu ndimo m'mene aliri anthu oipa. Nthaŵi zonse ali pabwino, ndipo amangolemera kosalekeza.
13
Ine ndasunga mtima wanga woyera, ndasamba m'manja kuwonetsa kuti ndine wosalakwa, koma zonsezi popanda phindu konse.
14
Pakuti ndapeza mavuto tsiku lonse, ndipo ndalangidwa m'maŵa mulimonse.
15
Ndikadati, “Ndilankhula monga amachitira iwowo,” ndikadakhala wosakhulupirika kwa zidzukulu zanu,
16
Koma pamene ndidalingalira zimenezi kuti ndizimvetse bwino, zidandiwonekera ngati nkhani yovuta,
17
mpaka nditakaloŵa m'malo opatulika a Mulungu, apo mpamene ndidaona mathero ake a anthuwo.
18
Zoonadi, Inu mumapondetsa anthu oipa pa malo oterera. Mumaŵagwetsa mpaka aonongeke.
19
Adzangoferatu ndi mantha, ndi kuwonongeka pa kamphindi kochepa.
20
Inu Ambuye, pamene mudzadzuka mudzaŵanyoza kotheratu, monga momwe munthu amanyozera maloto atadzuka m'maŵa.
21
Pamene paja ndinkavutika ndi maganizo, ndi kumamva cholasa mumtimamu,
22
ndinali wopusa wosamvetsa kanthu, ndinali ngati chilombo kwa Inu.
23
Koma chonsecho ndili ndi Inu nthaŵi zonse. Inu mumandigwira dzanja lamanja.
24
Mumandiwongolera ndi malangizo anu, pambuyo pake mudzandilandira ku ulemerero.
25
Nanga ndili ndi yani kumwamba kupatula Inu? Pansi pano palibe kanthu kena kamene ndimafuna, koma Inu nokha.
26
Thupi langa ndi mtima wanga zingafooke chotani, Mulungu ndiye mphamvu za mtima wanga ndiyenso wondigaŵira madalitso mpaka muyaya.
27
Onse amene ali kutali ndi Inu adzaonongeka, Inu mumaŵaononga amene ali osakhulupirika kwa Inu.
28
Koma ine kukhala pafupi ndi Mulungu kumandikomera. Ndatsimikiza zoti Ambuye ndiwo kothaŵira kwanga ndipo ndidzalalika ntchito zao zonse.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba