|
| 1 |
|
| Ndakatulo ya Asafu. Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu? |
|
| 2 |
|
| Kumbukirani anthu amene munawagula kalekale, fuko la cholowa chanu, limene Inu munaliwombola, phiri la Ziyoni, kumene inuyo mumakhala. |
|
| 3 |
|
| Tembenuzani mapazi kuloza ku mabwinja awa amuyaya chiwonongeko ichi chonse mdani wabweretsa pa malo opatulika. |
|
| 4 |
|
| Adani anu anabangula pa malo pamene Inu munkakumana nafe; anayimika mbendera zawo monga zizindikiro zachigonjetso. |
|
| 5 |
|
| Iwo anachita ngati anthu oti anyamula mbendera zawo kuti adule mitengo mʼnkhalango. |
|
| 6 |
|
| Kenaka anaphwanya ndi nkhwangwa ndi akasemasema awo zonse zimene tinapachika. |
|
| 7 |
|
| Iwo anatentha malo anu opatulika mpaka kuwagwetsa pansi; anadetsa malo okhalamo dzina lanu. |
|
| 8 |
|
| Ndipo anati mʼmitima yawo, “Tawatha kwathunthu.” Anatentha malo aliwonse amene Mulungu amapembedzedwerako mʼdzikomo. |
|
| 9 |
|
| Ife sitinapatsidwe chizindikiro chodabwitsa; palibe aneneri amene atsala ndipo palibe aliyense wa ife akudziwa kuti izi zidzatenga nthawi yayitali bwanji. |
|
| 10 |
|
| Kodi mpaka liti, mdani adzanyoze Inu Mulungu? Kodi amaliwongowa adzapeputsa dzina lanu kwamuyaya? |
|
| 11 |
|
| Chifukwa chiyani mukubweza dzanja lanu lamanja? Litulutseni kuchoka pachifuwa chanu ndipo muwawononge! |
|
| 12 |
|
| Koma Inu Mulungu, ndinu Mfumu yanga kuyambira kalekale; Mumabweretsa chipulumutso pa dziko lapansi. |
|
| 13 |
|
| Ndinu amene munagawa nyanja ndi mphamvu yanu; munathyola mitu ya zirombo za mʼmadzi. |
|
| 14 |
|
| Ndinu amene munaphwanya mitu ya Leviyatani ndi kuyipereka ngati chakudya cha zirombo za mʼchipululu. |
|
| 15 |
|
| Ndinu amene munatsekula akasupe ndi mitsinje, munawumitsa mitsinje imene siphwa nthawi zonse. |
|
| 16 |
|
| Masana ndi anu ndipo usiku ndi wanunso; Inuyo munakhazikitsa dzuwa ndi mwezi. |
|
| 17 |
|
| Ndinu amene munakhazikitsa malire onse a dziko lapansi; munakhazikitsa chilimwe ndi dzinja. |
|
| 18 |
|
| Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova, momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu. |
|
| 19 |
|
| Musapereke moyo wa nkhunda yanu ku zirombo zakuthengo; nthawi zonse musayiwale miyoyo ya anthu anu osautsidwa. |
|
| 20 |
|
| Mukumbukire pangano lanu, pakuti malo obisika a mʼdziko asanduka mochitira zachiwawa zochuluka. |
|
| 21 |
|
| Musalole kuti osautsidwa abwerere mwamanyazi; osauka ndi osowa atamande dzina lanu. |
|
| 22 |
|
| Dzukani Inu Mulungu ndipo dzitetezeni pa mlandu; kumbukirani momwe opusa akukunyozerani tsiku lonse. |
|
| 23 |
|
| Musalekerere phokoso la otsutsana nanu, chiwawa cha adani anu, chimene chikumveka kosalekeza. |
|
|
|
|