|
| 1 |
|
| Inu Mulungu, chifukwa chiyani mukutitaya mpaka muyaya? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutirira nkhosa za busa lanu ngati moto? |
|
| 2 |
|
| Kumbukirani mpingo wanu umene mudaupatula kuyambira kale, mtundu umene Inu mudauwombola kuti ukhale wanuwanu. Kumbukirani phiri la Ziyoni kumene Inu mudadzakhala. |
|
| 3 |
|
| Dzayendereni mabwinja oonongeka kwathunthuŵa. Adani aononga zinthu zonse za m'Nyumba yanu. |
|
| 4 |
|
| Adani anu abangula m'malo anu opatulika, adaikamo mbendera zao kusonyeza kuti agonjetsa. |
|
| 5 |
|
| Adadulamo zonse, monga momwe anthu amadulira mitengo m'nkhalango. |
|
| 6 |
|
| Pambuyo pake, ndi nsompho ndi nyundo, adakadzula zosemasema zonse. |
|
| 7 |
|
| Nyumba yanu adaitentha, malo amene Inu mumakhalako adaŵaipitsa poŵagwetsera pansi. |
|
| 8 |
|
| Mumtima mwao ankati, “Tiyeni tiŵagonjetse kotheratu.” Adatentha malo opatulika onse a Mulungu m'dzikomo. |
|
| 9 |
|
| Zizindikiro zonse za fuko lathu zaonongeka, kulibenso mneneri ndi mmodzi yemwe, palibe ndi mmodzi yemwe pakati pathu amene akudziŵa nthaŵi yodzatha zimenezi. |
|
| 10 |
|
| Inu Mulungu, adani athuŵa adzanyodolabe mpaka liti? Amaliwongowo adzanyozabe dzina lanu mpaka muyaya? |
|
| 11 |
|
| Chifukwa chiyani mukubisa dzanja lanu lotithandiza? Bwanji dzanja lanu lamanja likungokhala pachifuwa panu? |
|
| 12 |
|
| Komabe Inu Mulungu, ndinu mfumu yanga kuyambira kalekale. Ndinu amene mumagwira ntchito yopulumutsa pa dziko lonse lapansi. |
|
| 13 |
|
| Mudagaŵa Nyanja Yofiira ndi mphamvu zanu. Mudaphwanya mitu ya zilombo zam'madzi. |
|
| 14 |
|
| Mudatswanya mitu ya Leviyatani, chilombo cham'madzi chija, nkuitaya kuti ikhale chakudya cha zilombo zam'chipululu. |
|
| 15 |
|
| Mudatumphutsa akasupe ndi mifuleni, mudaumitsa mitsinje imene siiphwa. |
|
| 16 |
|
| Mudalenga usana ndi usiku. Mudaika mwezi ndi dzuŵa m'malo mwake. |
|
| 17 |
|
| Mudalemba malire a dziko lapansi, mudakhazikitsa chilimwe ndi dzinja. |
|
| 18 |
|
| Kumbukirani, Inu Chauta, kuti adani amakunyodolani, kuti anthu achipongwe amanyoza dzina lanu. |
|
| 19 |
|
| Musati mupereke moyo wa nkhunda yanu Israele ku zilombo zakuthengo. Musaiŵale mpaka muyaya moyo wa anthu anu osauka. |
|
| 20 |
|
| Kumbukirani chipangano chanu, pakuti malo obisika am'dziko asanduka mochitira zankhanza zambirimbiri. |
|
| 21 |
|
| Musalole kuti anthu oponderezedwa achite manyazi. Osauka ndi osoŵa akutamandeni. |
|
| 22 |
|
| Dzambatukani, Inu Mulungu, tiyeni mudziteteze pa mlandu wanuwo, kumbukirani kuti anthu amwano amakunyodolani tsiku lonse. |
|
| 23 |
|
| Musalekerere chiwawa cha amaliwongo anu, phokoso la adani anu limene likungokulirakulira nthaŵi zonse. |
|
|
|
|