×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 75

1
Tikuyamikani Inu, Mulungu; Tiyamika, pakuti dzina lanu liri pafupi; Afotokozera zodabwiza zanu,
2
Pakuona nyengo yace ndidzaweruza molunjika.
3
Lasungunuka dziko lapansi, ndi onse okhalamo; Ndinacirika mizati yace.
4
Ndinati kwa odzitamandira, Musamacita zodzitamandira; Ndi kwa oipa, Musamakweza nyanga;
5
Musamakwezetsa nyanga yanu; Musamalankhula ndi khosi louma.
6
Pakuti kukuzaku sikucokera kum'mawa, Kapena kumadzulo, kapena kucipululu,
7
Pakuti Mulungu ndiye woweruza; Acepsa wina, nakuza wina.
8
Pakuti m'dzanja la Yehova muli cikho; Ndi vinyo wace acita thobvu; Cidzala ndi zosanganizira, ndipo atsanulako: Indedi, oipa onse a pa dziko lapansi adzamwa Nadzagugudiza nsenga zace.
9
Koma ine ndidzalalikira kosalekeza, Ndidzayimbira zomlemekeza Mulungu wa Yakobo.
10
Ndipo ndidzatseteka nyanga zonse za oipa; Koma nyanga za wolungama zidzakwezeka.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba