Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo. Tikuthokoza Inu Mulungu, tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe, anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa. |
| 2 |
| Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera, ndine amene ndimaweruza mwachilungamo. |
| 3 |
| Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera, ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba. Sela |
| 4 |
| Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’ ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu. |
| 5 |
| Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba; musayankhule ndi khosi losololoka.’ ” |
| 6 |
| Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo kapena ku chipululu. |
| 7 |
| Koma ndi Mulungu amene amaweruza: Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina. |
| 8 |
| Mʼdzanja la Yehova muli chikho chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera; Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi amamwa ndi senga zake zonse. |
| 9 |
| Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya; ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo. |
| 10 |
| Ndidzadula nyanga za onse oyipa koma nyanga za olungama zidzakwezedwa. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/075.mp3
150
75