Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu. Mulungu amadziwika mu Yuda; dzina lake ndi lotchuka mu Israeli. |
| 2 |
| Tenti yake ili mu Salemu, malo ake okhalamo mu Ziyoni. |
| 3 |
| Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka, zishango ndi malupanga, zida zankhondo. Sela |
| 4 |
| Wolemekezeka ndinu, wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri. |
| 5 |
| Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma, Iwowo amagona tulo tawo totsiriza; palibe mmodzi wamphamvu amene angatukule manja ake. |
| 6 |
| Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo, kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi. |
| 7 |
| Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa. Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya? |
| 8 |
| Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo, ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete, |
| 9 |
| pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze, kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko. Sela |
| 10 |
| Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu. |
| 11 |
| Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse; anthu onse omuzungulira abweretse mphatso kwa Iye amene ayenera kuopedwa. |
| 12 |
| Iye amaswa mzimu wa olamulira; amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/076.mp3
150
76