×

Buku Loyera

MASALIMO 76

1
Mulungu ndi wodziŵika m'dziko la Yuda, dzina lake ndi lolemekezeka mu Israele.
2
Hema lake adalimanga ku Yerusalemu. Malo ake okhalamo ali kumeneko ku Ziyoni.
3
Kumeneko adathyola mivi youluzika, zishango, malupanga ndi zida zonse zankhondo za adani ake.
4
Inu Mulungu, mukuwonetsa ulemerero ndi mphamvu kupambana mapiri a zofunkha.
5
Mudalanda zofunkha za anthu olimba mtima, mudaŵagonetsa tulo tofa nato, ankhondo onse sankatha kuchita kanthu ndi manja ao.
6
Pamene mudaŵaopsa, Inu Mulungu wa Yakobe, onse okwera pa akavalo ndi akavalo ao omwe adagwa nangoti kakasi.
7
Zoonadi, Inu ndinu woopsa. Angathe kuima pamaso panu ndani pamene mkwiyo wanu wayaka?
8
Chiweruzo chanu mudachilengeza kumwamba, anthu a pa dziko lapansi adaopa nakhala chete,
9
pamene Inu Mulungu mudaimirira kuti muweruze anthu, ndi kupulumutsa opsinjidwa onse a pa dziko lapansi.
10
Zoonadi, mkwiyo wa anthu umabweretsa ulemu kwa Inu, opulumuka ku mkwiyowo mumaŵasunga pafupi ndi Inu.
11
Lumbirani kwa Chauta, Mulungu wanu, ndipo muchitedi zimene mwalumbirazo. Onse omzungulira abwere ndi mphatso kwa Iye amene ayenera kumuwopa,
12
ndiye amene amathetsa mphamvu akalonga ndipo amaopsa mafumu a pa dziko lapansi.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba