|
| 1 |
|
| Ndikulira mopemba kwa Mulungu, ndi mau okweza ndikufuula kwa Mulungu kuti andimve. |
|
| 2 |
|
| Pa tsiku lamavuto ndimafunafuna Ambuye. Usiku wonse ndimakweza manja anga ndi kupemphera kosalekeza. Mtima wanga umakana kuusangalatsa. |
|
| 3 |
|
| Ndikamalingalira za Mulungu, ndimangobuula mumtima. Ndikamasinkhasinkha za Iye, ndimataya mtima. |
|
| 4 |
|
| Mumagwira zikope zanga kuti ndisagone tulo. Ndikuvutika kwambiri kotero kuti sindingathe kulankhula. |
|
| 5 |
|
| Ndimalingalira za masiku akale, ndimakumbukira zaka zamakedzana. |
|
| 6 |
|
| Ndimasinkhasinkha mumtima mwanga usiku. Ndimadzifunsa ndi kufufuzafufuza mumtima mwanga. |
|
| 7 |
|
| Ndimati, “Kodi Ambuye adzandikana mpaka liti? Kodi sadzandikomeranso mtima? |
|
| 8 |
|
| Kodi chikondi chao chosasinthika chija chatheratu? Kodi malonjezo ao aja atha mpaka muyaya? |
|
| 9 |
|
| Kodi Mulungu waiŵala kukoma mtima kwake kuja? Kodi wakwiya ndi kuleka chifundo chake chija?” |
|
| 10 |
|
| “Chondiŵaŵa ndi chakuti, Mulungu Wopambanazonse wasintha mchitidwe wake.” |
|
| 11 |
|
| Komabe ndidzakumbukira ntchito zanu, Inu Chauta, inde, ndidzakumbukira zodabwitsa zanu zakalekale. |
|
| 12 |
|
| Ndidzasinkhasinkha za zonse zimene mwachita, ndidzalingalira za ntchito zanu zamphamvuzo. |
|
| 13 |
|
| Njira zanu, Inu Mulungu, nzoyera. Kodi alipo mulungu winanso wamkulu ngati Mulungu wathu? |
|
| 14 |
|
| Inu ndinu Mulungu amene mumachita zodabwitsa, amene mwaonetsa mphamvu zanu pakati pa mitundu ya anthu. |
|
| 15 |
|
| Mudaombola anthu anu ndi mkono wanu wamphamvu, ndiye kuti ana a Yakobe ndi Yosefe. |
|
| 16 |
|
| Pamene madzi adakuwonani, Inu Mulungu, pamene madzi adakuwonani, adachita mantha, inde, nyanja yakuya idanjenjemera. |
|
| 17 |
|
| Mitambo idachucha madzi, mumlengalenga mudachita bingu. Zing'aning'ani mbali ndi mbali. |
|
| 18 |
|
| Phokoso la bingu lanu lidamveka konsekonse, mphezi zanu zidaŵalitsa dziko lonse, dziko lapansi lidanjenjemera ndi kugwedezeka. |
|
| 19 |
|
| Inu mudadzera pa nyanja, njira yanu idadzera pa madzi akuya, komabe mapazi anu sadaoneke. |
|
| 20 |
|
| Mudatsogolera anthu anu ngati nkhosa kudzera mwa Mose ndi Aroni. |
|
|
|
|