|
| 1 |
|
| Tamverani, anthu anga, cilamulo canga; Cherezani khutu lanu mau a pakamwa panga. |
|
| 2 |
|
| Ndidzatsegula pakamwa panga mofanizira; Ndidzachula zinsinsi zoyambira kale; |
|
| 3 |
|
| Zimene tinazimva, ndi kuzidziwa, Ndipo makolo athu anatifotokozera. |
|
| 4 |
|
| Sitidzazibisira ana ao, Koma kufotokozera mbadwo ukudzawo zolemekeza za Yehova, Ndi mphamvu yace, ndi zodabwiza zace zimene anazicita. |
|
| 5 |
|
| Anakhazika mboni mwa Yakobo, Naika cilamulo mwa Israyeli, Ndizo analamulira atate athu, Akazidziwitse ana ao; |
|
| 6 |
|
| Kuti mbadwo ukudzawo udziwe, ndiwo ana amene akadzabadwa; Amene adzaimirira nadzafotokozera ana ao: |
|
| 7 |
|
| Ndi kuti ciyembekezo cao cikhale kwa Mulungu, Osaiwala zocita Mulungu, Koma kusunga malamulo ace ndiko. |
|
| 8 |
|
| Ndi kuti asange makolo ao, Ndiwo mbadwo woukirana ndi wopikisana ndi Mulungu; Mbadwo wosakonza mtima wao, Ndi mzimu wao sunakhazikika ndi Mulungu. |
|
| 9 |
|
| Ana a Efraimu okhala nazo zida, oponya nao mauta, Anabwerera m'mbuyo tsiku la nkhondo. |
|
| 10 |
|
| Sanasunga cipangano ca Mulungu, Nakana kuyenda m'cilamulo cace. |
|
| 11 |
|
| Ndipo anaiwala zocita Iye, Ndi zodabwiza zace zimene anawaonetsa. |
|
| 12 |
|
| Anacita codabwiza pamaso pa makolo ao, M'dziko la Aigupto ku cidikha ca Zoanu. |
|
| 13 |
|
| Anagawa nyanja nawapititsapo; Naimitsa madziwo ngati khoma. |
|
| 14 |
|
| Ndipo msana anawatsogolera ndi mtambo Ndi usiku wonse ndi kuunika kwa moto. |
|
| 15 |
|
| Anang'alula thanthwe m'cipululu, Ndipo anawamwetsa kocuruka monga m'madzi ozama. |
|
| 16 |
|
| Anaturukitsa mitsinje m'thanthwe, Inde anatsikitsa madzi ngati mitsinje. |
|
| 17 |
|
| Koma anaonjeza kuincimwira Iye, Kupikisana ndi Wam'mwambamwamba m'cipululu. |
|
| 18 |
|
| Ndipo anayesa Mulungu mumtimamwao Ndi kupempha cakudya monga mwa kulakalaka kwao. |
|
| 19 |
|
| Ndipo analankhula motsutsana ndi Mulungu; Anati, Kodi Mulungu akhoza kutikonzera podyera m'cipululu? |
|
| 20 |
|
| Taonani, anapanda thanthwe, ndi madzi anayendako Ndi mitsinje inasefuka; Kodi adzakhozanso kupatsa mkate? Kodi adzafunira anthu ace nyama? |
|
| 21 |
|
| Cifukwa cace Yehova anamva, nakwiya; Ndipo anayatsa moto pa Yakobo, Ndiponso mkwiyo unakwera pa Israyeli; |
|
| 22 |
|
| Popeza sanakhulupirira Mulungu, Osatama cipulumutso cace. |
|
| 23 |
|
| Koma analamulira mitambo iri m'mwamba, Natsegula m'makomo a kumwamba. |
|
| 24 |
|
| Ndipo anawabvumbitsira mana, adye, Nawapatsa tirigu wa kumwamba. |
|
| 25 |
|
| Yense anadya mkate wa omveka: Anawatumizira cakudya cofikira, |
|
| 26 |
|
| Anaombetsa m'mwamba mphepo ya kum'mawa: Natsogoza mwela ndi mphamvu yace. |
|
| 27 |
|
| Ndipo anawabvumbitsira nyama ngati pfumbi, Ndi mbalame zouluka ngati mcenga wa kunyanja: |
|
| 28 |
|
| Ndipo anazigwetsa pakati pa misasa yao, Pozungulira pokhala iwo. |
|
| 29 |
|
| Potero anadya nakhuta kwambiri; Ndipo anawapatsa cokhumba iwo. |
|
| 30 |
|
| Asanathe naco cokhumba cao, Cakudya cao ciri m'kamwa mwao, |
|
| 31 |
|
| Pamenepo mkwiyo wa Mulungu unawaukira, Ndipo anapha mwa onenepa ao, Nagwetsa osankhika a Israyeli. |
|
| 32 |
|
| Cingakhale ici conse anacimwanso, Osabvomereza zodabwiza zace. |
|
| 33 |
|
| Potero anathera masiku ao ndi zopanda pace, Ndi zaka zao mwa mantha. |
|
| 34 |
|
| Pamene anawapha ndipo anamfuna Iye; Nabwerera, nafunitsitsa Mulungu, |
|
| 35 |
|
| Ndipo anakumbukila kuti Mulungu ndiye thanthwe lao, Ndi Mulungu Wam'mwambamwamba Mombolo wao. |
|
| 36 |
|
| Koma anamsyasyalika pakamwa pao, Namnamiza ndi lilime lao. |
|
| 37 |
|
| Popeza mtima wao sunakonzekera Iye, Ndipo sanakhazikika m'cipangano cace. |
|
| 38 |
|
| Koma Iye pokhala ngwa cifundo, Anakhululukira coipa, osawaononga; Nabweza mkwiyo wace kawiri kawiri, Sanautsa ukali wace wonse. |
|
| 39 |
|
| Ndipo anakumbukira kuti iwo ndiwo anthu; Mphepo yopita yosabweranso. |
|
| 40 |
|
| Kawiri kawiri nanga anapikisana ndi Iye kucigwako, Nammvetsa cisoni m'cipululu. |
|
| 41 |
|
| Pakuti anabwerera m'mbuyo, nayesa Mulungu, Nacepsa Woyerayo wa Israyeli. |
|
| 42 |
|
| Sanakumbukila dzanja lace, Tsikuli anawaombola kwa msautsi. |
|
| 43 |
|
| Amene anaika zizindikilo zace m'Aigupto, Ndi zodabwiza zace ku cidikha ca Zoanu; |
|
| 44 |
|
| Nasanduliza nyanja yao mwazi, Ndi mitsinje yao, kuti sangakhoze kumwa. |
|
| 45 |
|
| Anawatumizira pakati pao mitambo ya nchenche zakuwatha; Ndi acule akuwaononga. |
|
| 46 |
|
| Ndipo anapatsa mphuci dzinthu dzao, Ndi dzombe nchito yao. |
|
| 47 |
|
| Anapha mphesa zao ndi matalala, Ndi mikuyu yao ndi cisanu. |
|
| 48 |
|
| Naperekanso zoweta zao kwa matalala, Ndi ng'ombe zao kwa mphezi. |
|
| 49 |
|
| Anawatumizira mkwiyo wace wotentha, Kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, Ndizo gulu la amithenga ocita zoipa. |
|
| 50 |
|
| Analambulira mkwiyo wace njira; Sanalekerera moyo wao usafe, Koma anapereka moyo wao kumliri; |
|
| 51 |
|
| Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Aigupto, Ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu: |
|
| 52 |
|
| Koma anaturutsa anthu ace ngati nkhosa, Nawatsogoza ngati gulu la zoweta m'cipululu. |
|
| 53 |
|
| Ndipo anawatsogolera mokhulupirika, Kotero kuti sanaopa; Koma nyanja inamiza adani ao. |
|
| 54 |
|
| Ndipo anawafikitsa ku malire a malo ace oyera, Ku phiri ili, dzanja lamanja lace lidaligula. |
|
| 55 |
|
| Ndipo anapitikitsa amitundu pamaso pao, Nawagawira colowa cao, ndi muyeso, Nakhalitsa mafuko a Israyeli m'mahema mwao. |
|
| 56 |
|
| Koma anamuyesa napikisana ndi Mulungu Wam'mwambamwamba, Osasunga mboni zace; |
|
| 57 |
|
| Koma anabwerera m'mbuyo, nacita zosakhulupirika monga makolo ao: Anapatuka ngati uta wolenda, |
|
| 58 |
|
| Ndipo anautsa mtima wace ndi malo amsanje ao, Namcititsa nsanje ndi mafano osema. |
|
| 59 |
|
| Pakumva ici Mulungu, anakwiya, Nanyozatu Israyeli; |
|
| 60 |
|
| Ndipo anacokera cokhalamo ca ku Silo, Cihemaco adacimanga mwa anthu; |
|
| 61 |
|
| Napereka mphamvu yace m'ukapolo, Ndi ulemerero wace m'dzanja la msautsi. |
|
| 62 |
|
| Naperekanso anthu ace kwa lupanga; Nakwiya naco colandira cace. |
|
| 63 |
|
| Moto unapsereza anyamata ao; Ndi anamwali ao sanalemekezeka. |
|
| 64 |
|
| Ansembe ao anagwa ndi lupanga; Ndipo amasiye ao sanacita maliro. |
|
| 65 |
|
| Pamenepo Ambuye anauka ngati wam'tulo; Ngati ciphona cakucita nthungululu ndi vinyo. |
|
| 66 |
|
| Ndipo anapanda otsutsana naye kumbuyo; Nawapereka akhale otonzeka kosatha. |
|
| 67 |
|
| Tero anakana hema wa Yosefe; Ndipo sanasankha pfuko la Efraimu; |
|
| 68 |
|
| Koma anasankha pfuko la Yuda, Phiri la Ziyoni limene analikonda. |
|
| 69 |
|
| Ndipo anamanga malo oyera ace ngati kaphiri, Monga dziko lapansi limene analikhazikitsa kosatha. |
|
| 70 |
|
| Ndipo anasankha Davide mtumiki wace, Namtenga ku makola a nkhosa: |
|
| 71 |
|
| Anamtenga kuja anatsata zoyamwitsa, Awete Yakobo, anthu ace, ndi Israyeli, colandira cace. |
|
| 72 |
|
| Potero anawaweta monga mwa mtima wace wangwiro; Nawatsogolera ndi luso la manja ace. |
|
|
|
|