Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo la Asafu. Inu Mulungu, anthu a mitundu ina alowerera mʼcholowa chanu; ayipitsa Nyumba yanu yoyera, asandutsa Yerusalemu kukhala bwinja. |
| 2 |
| Iwo anapereka mitembo ya atumiki anu kwa mbalame zamlengalenga ngati chakudya, matupi a oyera mtima anu kwa zirombo za dziko lapansi. |
| 3 |
| Akhetsa magazi monga madzi kuzungulira Yerusalemu yense, ndipo palibe wina woti ayike mʼmanda anthu akufa. |
| 4 |
| Ife ndife chinthu chonyozeka kwa anansi athu, choseketsa ndi cholalatiridwa kwa iwo amene atizungulira. |
| 5 |
| Mpaka liti Inu Yehova? Kodi mudzakwiya mpaka muyaya? Kodi mpaka liti nsanje yanu idzayaka ngati moto? |
| 6 |
| Khuthulirani ukali wanu pa anthu a mitundu ina amene sakudziwani Inu, pa maufumu amene sayitana pa dzina lanu; |
| 7 |
| pakuti iwo ameza Yakobo ndi kuwononga dziko lawo. |
| 8 |
| Musatilange chifukwa cha machimo a makolo athu chifundo chanu chibwere msanga kukumana nafe, pakuti tili ndi chosowa chachikulu. |
| 9 |
| Tithandizeni Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, chifukwa cha ulemerero wa dzina lanu; tipulumutseni ndi kutikhululukira machimo athu chifukwa cha dzina lanu. |
| 10 |
| Chifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuti, “Ali kuti Mulungu wawo?” Ife tikuona, zidziwike pakati pa anthu a mitundu ina kuti mumabwezera chilango chifukwa cha magazi amene anakhetsedwa a atumiki anu. |
| 11 |
| Kubuwula kwa anthu a mʼndende kufike pamaso panu; ndi mphamvu ya dzanja lanu muwasunge amene aweruzidwa kuti aphedwe. |
| 12 |
| Mubwezere kwa anansi athu kasanu nʼkawiri kunyoza kumene ananyoza Inu Ambuye. |
| 13 |
| Pamenepo ife anthu anu, nkhosa za pabusa panu, tidzakutamandani kwamuyaya, kuchokera mʼbado ndi mʼbado tidzafotokoza za matamando anu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/079.mp3
150
79