×

Buku Loyera

MASALIMO 80

1
Imvani, Inu Mbusa wa Israele, Inu amene mumatsogolera anthu a Yosefe ngati gulu la nkhosa. Inu amene mumakhala pa akerubi ngati pa mpando wanu wachifumu,
2
dziwonetseni kwa mafuko a Efuremu ndi Benjamini ndi Manase. Onetsani mphamvu zanu, ndipo mubwere kudzatipulumutsa.
3
Inu Mulungu, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yanu yokondwa, ndipo ife tidzapulumuka.
4
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, mudzakwiyira mapemphero a anthu anu mpaka liti?
5
Mwaŵadyetsa chisoni ngati chakudya, mwaŵapatsa misozi ngati chakumwa.
6
Mwaŵasandutsa chinthu chonyozeka kwa anzathu a mitundu ina, ndipo adani athu akakhala pamodzi, amangotiseka.
7
Inu Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale, mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke.
8
Mudatulutsa mpesa wanu Israele m'dziko la Ejipito. Mudapirikitsa mitundu ina ya anthu kuti muubzale mpesawo.
9
Mudaulimira munda mpesawo, udamera mizu yozama, nudzaza m'dzikolo.
10
Mapiri adaphimbidwa ndi mthunzi wake, mikungudza yaikulu yomwe idaphimbidwa ndi nthambi zake.
11
Nthambizo zidafika mpaka ku nyanja yaikulu yakuzambwe, ndipo mphukira zake mpaka ku mtsinje waukulu wakuvuma.
12
Nanga chifukwa chiyani mwagumula mpanda wake, kuti opita m'njira azithyola nawo zipatso zake?
13
Nguluŵe zam'nkhalango zimauwononga, ndipo zonse zoyenda m'thengo zimaudya.
14
Mutembenukirenso kwa ife, Inu Mulungu Wamphamvuzonse, muyang'ane Inu okhala kumwamba, ndipo muwone. Samalani mpesawo,
15
mtengo woyambirira umene Inu mudaubzala ndi dzanja lanu lamanja.
16
Adani athu autentha, augwetsa pansi. Ayang'aneni iwowo mokwiya ndi kuŵaononga.
17
Koma ndi dzanja lanu muteteze anthu amene mudaŵasankha, anthu amene Inu nomwe mwaŵalimbikitsa kuti akutumikireni.
18
Tsono sitidzakusiyaninso, tipatseni moyo, ndipo tidzatama dzina lanu mopemba.
19
Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, tibwezereni mwakale. Mutiwonetse nkhope yoŵala, kuti ife tipulumuke.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba