Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu. Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu; Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo! |
| 2 |
| Yambani nyimbo, imbani tambolini imbani pangwe wolira bwino ndi zeze. |
| 3 |
| Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano, ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando; |
| 4 |
| ili ndi lamulo kwa Israeli, langizo la Mulungu wa Yakobo. |
| 5 |
| Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto, kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe. |
| 6 |
| Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo; Manja awo anamasulidwa mʼdengu. |
| 7 |
| Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani, ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu; ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba. Sela |
| 8 |
| “Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli! |
| 9 |
| Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu; musadzagwadire mulungu wina. |
| 10 |
| Ine ndine Yehova Mulungu wanu, amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto. Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani. |
| 11 |
| “Koma anthu anga sanandimvere; Israeli sanandigonjere. |
| 12 |
| Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo kuti atsate zimene ankafuna. |
| 13 |
| “Anthu anga akanangondimvera, Israeli akanatsatira njira zanga, |
| 14 |
| nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo! |
| 15 |
| Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake, ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale. |
| 16 |
| Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri; ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/081.mp3
150
81