×

Buku Loyera

MASALIMO 82

1
Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba. Akugamula mlandu milungu ya pansi pano.
2
Akuti, “Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti? Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa?
3
Inu tetezani anthu ofooka ndi amasiye mwachilungamo. Weruzani molungama ozunzika ndi amphaŵi.
4
“Landitsani ofooka ndi osoŵa. Apulumutseni kwa anthu oipa.”
5
Iwo sadziŵa kanthu ndiponso alibe nzeru, amangoyenda m'chimbulimbuli. Maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6
Ine ndikuti, “Inu ndinu milungu, nonsenu ndinu ana a Mulungu Wopambanazonse.
7
Komabe mudzafa ngati anthu onse, ndipo mudzagwa ngati kalonga wina aliyense.”
8
Dzambatukani, Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi, popeza kuti mitundu yonse ya anthu ndi yanu.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba