Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Nyimbo. Salimo la Asafu. Inu Mulungu musakhale chete; musangoti phee, Mulungu musangoti duu. |
| 2 |
| Onani adani anu akuchita chiwawa, amene amadana nanu autsa mitu yawo. |
| 3 |
| Mochenjera iwo akukambirana za chiwembu kutsutsana ndi anthu anu; Iwo akukonzekera kutsutsana ndi omwe mumawakonda. |
| 4 |
| Iwo akunena kuti, “Bwerani” akutero, “Tiyeni tiwononge mtundu wonsewu kuti dzina la Israeli lisakumbukikenso.” |
| 5 |
| Ndi mtima umodzi akukonzekera chiwembu; Iwo achita mgwirizano kutsutsana nanu: |
| 6 |
| Matenti a Edomu ndi Aismaeli, Mowabu ndi Ahagiri, |
| 7 |
| Agebala, Aamoni ndi Aamaleki, Afilisti, pamodzi ndi anthu a ku Turo. |
| 8 |
| Ngakhalenso Aasiriya aphatikizana nawo kupereka mphamvu kwa ana a Loti. Sela |
| 9 |
| Muwachitire zomwe munachitira Amidiyani, monga munachitira Sisera ndi Yabini ku mtsinje wa Kisoni. |
| 10 |
| Amene anawonongedwa ku Endori ndi kukhala ngati zinyalala. |
| 11 |
| Anthu awo otchuka muwachite zomwe munachita Orebu ndi Zeebu ana a mafumu muwachite zomwe munachita Zeba ndi Zalimuna, |
| 12 |
| amene anati, “Tiyeni tilande dziko la msipu la Mulungu.” |
| 13 |
| Muwasandutse fumbi lowuluka, Inu Mulungu wanga, ngati mankhusu owuluka ndi mphepo. |
| 14 |
| Monga moto umatentha nkhalango, kapena malawi a moto kuyatsa phiri, |
| 15 |
| kotero muwathamangitse ndi mphepo yamkuntho, ndi kuwachititsa mantha ndi namondwe. |
| 16 |
| Muphimbe nkhope zawo ndi manyazi kuti adzafunefune dzina lanu Yehova. |
| 17 |
| Achite manyazi ndi mantha nthawi zonse; awonongeke mwa manyazi. |
| 18 |
| Adziwe kuti Inu amene dzina lanu ndi Yehova, ndinu nokha Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/083.mp3
150
83