Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a Gititi. Salimo la ana a Kora. Malo anu okhalamo ndi okomadi, Inu Yehova Wamphamvuzonse! |
| 2 |
| Moyo wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufuna mabwalo a Yehova; Mtima wanga ndi thupi langa zikufuwulira Mulungu wamoyo. |
| 3 |
| Ngakhale timba wapeza nyumba yokhalamo, ndiponso namzeze wadzipezera yekha chisa, kumene amagonekako ana ake pafupi ndi guwa lanu la nsembe, Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga. |
| 4 |
| Odala amene amakhala mʼNyumba yanu; nthawi zonse amakutamandani. Sela |
| 5 |
| Odala amene mphamvu yawo ili mwa Inu, mitima yawo ikufunitsitsa kuyenda mʼmisewu yopita ku Ziyoni. |
| 6 |
| Pamene akudutsa chigwa cha Baka, amachisandutsa malo a akasupe; mvula ya chizimalupsa imadzazanso mayiwe ake. |
| 7 |
| Iwo amanka nakulirakulira mphamvu mpaka aliyense ataonekera pamaso pa Mulungu mu Ziyoni. |
| 8 |
| Imvani pemphero langa, Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse; mvereni Inu Mulungu wa Yakobo. Sela |
| 9 |
| Yangʼanani chishango chathu, Inu Mulungu; yangʼanani mokoma mtima pa wodzozedwa wanu. |
| 10 |
| Nʼkwabwino kukhala mʼmabwalo anu tsiku limodzi kuposa kukhala kwina kwake kwa zaka 1,000; Ine ndingakonde kukhala mlonda wa pa khomo la Nyumba ya Mulungu wanga kuposa kukhala mʼmatenti a anthu oyipa. |
| 11 |
| Pakuti Yehova Mulungu ndi dzuwa ndi chishango; Yehova amapereka chisomo ndi ulemu; Iye sawamana zinthu zabwino iwo amene amayenda mwangwiro. |
| 12 |
| Inu Yehova Wamphamvuzonse, wodala ndi munthu amene amakhulupirira Inu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/084.mp3
150
84