Buku Loyera
|
| 1 |
| Malo amene mumakhalamo, Inu Chauta Wamphamvuzonse, ndi okoma kwambiri. |
| 2 |
| Mtima wanga ukulakalaka, mpaka kukomoka, kufunitsitsa kuwona mabwalo a Chauta. Inu Mulungu wamoyo, ndikukuimbirani mwachimwemwe ndi mtima wanga wonse. |
| 3 |
| Ngakhale timba amapeza malo okhalapo, nayenso namzeze amamanga chisa chake m'mene amagonekamo ana ake, pafupi ndi maguwa anu, Inu Chauta Wamphamvuzonse, Mfumu yanga ndi Mulungu wanga. |
| 4 |
| Ngodala anthu amene amakhala m'Nyumba mwanu, namaimba nyimbo zotamanda Inu nthaŵi zonse. |
| 5 |
| Ngodala anthu amene mphamvu zao nzochokera kwa Inu, amene m'mitima mwao amafunitsitsa kudzera m'miseu yopita ku Ziyoni. |
| 6 |
| Akamadutsa chigwa cha Baka chopanda madzi, amachisandutsa malo a akasupe, mvula yachizimalupsa imachidzaza ndi zithaphwi. |
| 7 |
| Mphamvu zao zimanka zichulukirachulukira. Mulungu wa milungu adzaoneka m'Ziyoni. |
| 8 |
| Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse, imvani pemphero langa. Tcherani khutu, Inu Mulungu wa Yakobe. |
| 9 |
| Inu Mulungu, ndinu chishango chathu, yang'anani nkhope ya wodzozedwa wanu. |
| 10 |
| Kukhala tsiku limodzi m'mabwalo anu nkwabwino kwambiri kupambana kukhala masiku ambiri kwina kulikonse. Nkadakonda kukhala wapakhomo wa Nyumba ya Mulungu wanga kupambana kukhala m'nyumba za anthu oipa. |
| 11 |
| Pakuti Chauta ndiye dzuŵa ndi chishango, amatichitira chifundo ndi kutipatsa ulemu. Chauta saŵamana zabwino anthu oyenda molungama. |
| 12 |
| Inu Chauta Wamphamvuzonse, ngwodala munthu woika chikhulupiriro chake pa Inu. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/084.mp3
150
84