Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la ana a Kora. Yehova munakomera mtima dziko lanu; munabwezeretsa ulemerero wa Yakobo. |
| 2 |
| Munakhululukira mphulupulu za anthu anu ndi kuphimba machimo awo onse. Sela |
| 3 |
| Munayika pambali ukali wanu wonse ndi kutembenuka kuchoka ku mkwiyo wanu woopsa. |
| 4 |
| Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu. |
| 5 |
| Kodi mudzatikwiyira mpaka liti? Kodi mudzapitiriza kukwiya pa mibado yathu yonse? |
| 6 |
| Kodi simudzatitsitsimutsanso, kuti anthu anu asangalale mwa Inu? |
| 7 |
| Tionetseni chikondi chanu chosatha, Inu Yehova, ndipo tipatseni chipulumutso chanu. |
| 8 |
| Ndidzamvetsera zimene Yehova Mulungu adzanena; Iye amalonjeza mtendere kwa anthu ake, oyera mtima ake, koma musawalole kuti abwerere ku zopusa. |
| 9 |
| Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye, kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu. |
| 10 |
| Chikondi ndi kukhulupirika zimakumana pamodzi; chilungamo ndi mtendere zimapsompsonana. |
| 11 |
| Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi, ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba. |
| 12 |
| Ndithu Yehova adzapereka chimene chili chabwino, ndipo dziko lathu lidzapereka zokolola zake. |
| 13 |
| Wolungama amapita patsogolo pake ndi kukonza njira za mapazi ake. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/085.mp3
150
85