Buku Loyera
|
| 1 |
| Inu Chauta, mudakomera mtima dziko lanu, mudaŵakhazikanso pabwino a m'banja la Yakobe. |
| 2 |
| Mudakhululukira machimo a anthu anu, mudafafaniza zolakwa zao zonse. |
| 3 |
| Mudaleka ndithu ukali wanu woopsa, mudaletsa mkwiyo wanu woyaka moto. |
| 4 |
| Mutibwezerenso mwakale, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu. |
| 5 |
| Kodi mudzakhalabe mukutikwiyira mpaka muyaya? Kodi mudzapitiriza kukwiya mpaka pa mibadwo yathu yonse? |
| 6 |
| Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti ife anthu anu tikondwere mwa Inu? |
| 7 |
| Tiwonetseni chikondi chanu chosasinthika, Inu Chauta, ndipo mutipulumutse. |
| 8 |
| Ndimve zimene Chauta adzalankhula, chifukwa adzalankhula za mtendere kwa anthu ake, kwa anthu ake oyera mtima, ngati sabwereranso ku zopusa zao. |
| 9 |
| Zoonadi, Mulungu ali wokonzekera kuti apulumutse amene amamuwopa, kuti ulemerero wake ukhale m'dziko lathu. |
| 10 |
| Chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika zidzakumana. Chilungamo ndi mtendere zidzagwirizana. |
| 11 |
| Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano, ndipo Mulungu wakumwamba adzaŵalungamitsa. |
| 12 |
| Inde, Chauta adzapereka zabwino, ndipo dziko lathu lidzabereka zokolola zambiri. |
| 13 |
| Mulungu ndi wolungama chikhalire, chilungamo chake chimaongolera zochita zake zonse. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/085.mp3
150
85