|
| 1 |
|
| Tcherani khutu, Inu Chauta, ndipo mundiyankhe, pakuti ndine wosauka ndi wosoŵa. |
|
| 2 |
|
| Sungani moyo wanga, pakuti ndine womvera Inu. Pulumutseni ine mtumiki wanu amene ndimadalira Inu. Inu ndinu Mulungu wanga. |
|
| 3 |
|
| Mundikomere mtima, Inu Ambuye, popeza kuti ndimalirira Inu tsiku lonse. |
|
| 4 |
|
| Sangalatsani mtima wa ine mtumiki wanu, pakuti ndikupereka mtima wanga kwa Inu Ambuye. |
|
| 5 |
|
| Inu Ambuye ndinu abwino, ndipo mumakhululukira anthu anu. Chikondi chanu chosasinthika ndi chachikulu kwa onse amene amakupembedzani. |
|
| 6 |
|
| Tcherani khutu, Inu Chauta, kuti mumve pemphero langa. Mverani kulira kwanga kopemba. |
|
| 7 |
|
| Pa tsiku lamavuto ndimakuitanani, pakuti mumayankha mapemphero anga. |
|
| 8 |
|
| Pakati pa milungu palibe ndi mmodzi yemwe wolingana nanu, Inu Ambuye, palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu. |
|
| 9 |
|
| Mitundu yonse ya anthu imene mwailenga idzabwera, idzakuŵeramirani, Inu Ambuye, ndipo idzalemekeza ukulu wanu. |
|
| 10 |
|
| Pakuti Inu ndinu wamkulu, mumachita zinthu zodabwitsa, Inu nokha ndinu Mulungu. |
|
| 11 |
|
| Phunzitseni njira zanu, Inu Chauta, kuti ndiziyenda m'zoona zanu. Mundipatse mtima wosagaŵikana, kuti ndiziwopa dzina lanu. |
|
| 12 |
|
| Inu Ambuye, Mulungu wanga, ndikukuthokozani ndi mtima wanga wonse, ndidzalemekeza ukulu wanu mpaka muyaya. |
|
| 13 |
|
| Paja chikondi chanu chosasinthika kwa ine nchachikulu, Mwandipulumutsa ku malo akuya a anthu akufa. |
|
| 14 |
|
| Inu Mulungu, anthu achipongwe andiwukira. Anthu opanda chifundo akufunafuna moyo wanga ndipo sasamala za Inu. |
|
| 15 |
|
| Koma Inu Ambuye, ndinu Mulungu wachifundo ndinu Mulungu wokoma mtima, wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi chosasinthika, ndi wokhulupirika kotheratu. |
|
| 16 |
|
| Mundiyang'ane ndipo mundichitire chifundo. Mundipatse mphamvu zanu ine mtumiki wanu, mundipulumutse ine mwana wa mdzakazi wanu. |
|
| 17 |
|
| Mundiwonetse chizindikiro chakuti mumandikomera mtima, kuti odana nane achite manyazi. Adzaona kuti Inu Chauta mwandithandiza ndi kundilimbitsa mtima. |
|
|
|
|