×

Buku Loyera

MASALIMO 87

1
Mzinda umene Chauta adamanga maziko ake, uli pa phiri loyera.
2
Chauta amakonda mzinda wa Ziyoni amaukonda kupambana kwina kulikonse kumene zidzukulu za Yakobe zimakhala.
3
Iwe mzinda wa Mulungu, anthu amakamba zambiri zotamanda iwe.
4
Amati, “Pakati pa amene amandidziŵa, ndikutchula Rahabu ndi Babiloni. Ponena za dziko la Filistiya, Tiro ndi Etiopiya, anthu amati, ‘Uje adabadwira kumeneko.’ ”
5
Koma ponena za Ziyoni adzati, “Onse adabadwira kumeneko,” chifukwa Wopambanazonse mwini wake ndiye amene adzaulimbitsa mzindawo.
6
Tsono polemba maina a mitundu yonse ya anthu, Chauta adzati, “Wakutiwakuti adabadwira ku Ziyoni.”
7
Oimba ndi ovina adzati, “Ziyoni ndiwe kasupe wa madalitso athu onse.”
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba