Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Yehova, Mulungu wa cipulumutso canga, Ndinapfuula pamaso panu usana ndi usiku, |
| 2 |
| Pemphero langa lidze pamaso panu; Mundicherere khutu kukuwa kwanga: |
| 3 |
| Pakuti mzimu wanga wadzala nao mabvuto, Ndi moyo wanga wayandikira kumanda. |
| 4 |
| Anandiwerenga pamodzi nao otsikira kudzenje; Ndakhala ngati munthu wopanda mphamvu: |
| 5 |
| Wotayika pakati pa akufa, Ngati ophedwa akugona m'manda, Amene simuwakumbukilanso; Ndipo anawadula kusiyana ndi dzanja lanu. |
| 6 |
| Munandiika kunsi kwa dzenje, Kuti mdima, kozama. |
| 7 |
| Mkwiyo wanu utsamira pa ine, Ndipo munandizunza ine ndi mafunde anu onse. |
| 8 |
| Munandisiyanitsira wodziwana nane kutali; Munandiika ndiwakhalire conyansa: Ananditsekereza osakhoza kuturuka ine. |
| 9 |
| Diso langa lapuwala cifukwa ca kuzunzika kwanga: Ndimaitana Inu, Yehova, tsiku lonse; Nditambalitsira manja anga kwa Inu. |
| 10 |
| Kodi mudzacitira akufa zodabwiza? Kodi adzaukanso otisiyawo, ndi kukulemekezani? |
| 11 |
| Adzafotokozera cifundo canu kumanda kodi, Cikhulupiriko canu ku malo a cionongeko? |
| 12 |
| Zodabwiza zanu zidzadziwika mumdima kodi, Ndi cilungamo canu m'dziko la ciiwaliko? |
| 13 |
| Koma ndinapfuulira kwa Inu, Yehova, Ndipo pemphero langa likumika Inu mamawa. |
| 14 |
| Yehova mutayiranji moyo wanga? Ndi kundibisira nkhope yanu? |
| 15 |
| Wozunzika ine ndi wofuna kufa kuyambira ubwana wanga; Posenza zoopsa zanu, ndithedwa nzeru. |
| 16 |
| Kuzaza kwanu kwandimiza; Zoopsa zanu zinandiononga, |
| 17 |
| Zinandizungulira ngati madzi tsiku lonse; Zinandizinga pamodzi. |
| 18 |
| Munandicotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa, Odziwana nane akhala kumdima. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/psalms/088.mp3
150
88