|
| 1 |
|
| Inu Chauta, Mpulumutsi wanga, ndimalirira Inu usana ndi usiku, kuti mundithandize. |
|
| 2 |
|
| Pemphero langa lifike kwa Inu, tcherani khutu kuti mumve kulira kwanga. |
|
| 3 |
|
| Pakuti mtima wanga ndi wodzaza ndi mavuto, moyo wanga ukuyandikira ku malo a anthu akufa. |
|
| 4 |
|
| Ndikuŵerengedwa pamodzi ndi anthu otsikira ku manda. Ndasanduka munthu wopanda mphamvu. |
|
| 5 |
|
| Ndili ngati munthu womsiya yekha pakati pa anthu akufa, ngati munthu wophedwa amene wagona m'manda. Ndili ngati anthu amene Inu simuŵakumbukiranso, popeza kuti ndi ochotsedwa m'manja mwanu. |
|
| 6 |
|
| Inu mwandiika pansi penipeni pa dzenje m'malo akuya a mdima wandiweyani. |
|
| 7 |
|
| Mkwiyo wanu ukundipsinja, mukundimiza ndi mafunde anu onse. |
|
| 8 |
|
| Inu mwachititsa kuti anzanga azindithaŵa, mwandisandutsa chinthu choŵanyansa. Ndatsekerezedwa kotero kuti sindingathe kuthaŵa. |
|
| 9 |
|
| M'maso mwanga mwada ndi chisoni. Tsiku ndi tsiku ndimakuitanani, Inu Chauta, Ndimakweza manja anga kwa Inu. |
|
| 10 |
|
| Kodi zodabwitsa mumachitira anthu akufa? Kodi iwowo nkuuka kuti akutamandeni? |
|
| 11 |
|
| Kodi chikondi chanu chosasinthikacho amachilalikira ku manda? Kodi amasimba za kukhulupirika kwanu ku malo achiwonongeko? |
|
| 12 |
|
| Kodi zodabwitsa zanu zimadziŵika mu mdima? Ndani angadziŵe za chithandizo chanu chopulumutsa m'dziko la anthu oiŵalika? |
|
| 13 |
|
| Koma ine ndimalirira Inu Chauta, m'maŵa pemphero langa limakafika kwa Inu. |
|
| 14 |
|
| Inu Chauta, chifukwa chiyani mukunditaya? Chifukwa chiyani mukundibisira nkhope yanu? |
|
| 15 |
|
| Kuyambira ubwana wanga mpaka kukula, ndakhala ndikupirira zilango zanu pozunzika mpaka pafupi kufa, tsopano ndatheratu. |
|
| 16 |
|
| Mkwiyo wanu wandimiza, moyo wanga waonongekeratu ndi ukali wanu woopsa. |
|
| 17 |
|
| Zonsezi zimandizinga tsiku lonse ngati chigumula, zanditsekereza kwathunthu. |
|
| 18 |
|
| Inu mwathaŵitsa anthu ondikonda ndi abwenzi anga, mdima wokha ndiye mnzanga amene wanditsalira. |
|
|
|
|