Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Iye amene amakhala mu mthunzi wa Wammwambamwamba adzapuma mu mthunzi wa Wamphamvuzonse. |
| 2 |
| Ndidzanena za Yehova, “Iye ndiye pothawira panga ndi linga langa, Mulungu wanga amene ndimadalira.” |
| 3 |
| Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa mlenje ndi ku mliri woopsa; |
| 4 |
| Adzakuphimba ndi nthenga zake, ndipo udzapeza malo othawira mʼmapikomo; kukhulupirika kwake kudzakhala chishango chako ndi lihawo. |
| 5 |
| Sudzachita mantha ndi zoopsa za usiku, kapena muvi wowuluka masana, |
| 6 |
| kapena mliri umene umayenda mu mdima, kapena zowononga za pa nthawi ya masana. |
| 7 |
| Anthu 1,000 atha kufa pambali pako, anthu 10,000 kudzanja lako lamanja, koma zoopsazo sizidzafika pafupi ndi iwe. |
| 8 |
| Udzapenya ndi maso ako ndipo udzaona mmene anthu oyipa amalangidwira. |
| 9 |
| Pakuti wasankha Wammwambamwamba kukhala malo ako okhalamo; wavomera Yehova kukhala kothawira kwako. |
| 10 |
| Choncho palibe choyipa chimene chidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi tenti yako. |
| 11 |
| Pakuti adzalamulira angelo ake za iwe, kuti akutchinjirize mosamala pa njira zako zonse; |
| 12 |
| ndipo adzakunyamula ndi manja awo, kuti phazi lako lisagunde pa mwala. |
| 13 |
| Udzapondaponda mkango ndi njoka, udzapondereza mkango wamphamvu ndiponso chinjoka. |
| 14 |
| “Chifukwa iye amandikonda,” akutero Yehova, “Ndidzamulanditsa; ndidzamuteteza pakuti wavomereza dzina langa. |
| 15 |
| Adzandiyitana, ndipo ndidzamuyankha; ndidzakhala naye pa mavuto, ndidzamupulumutsa ndi kumulemekeza. |
| 16 |
| Ndidzamupatsa moyo wautali ndi kumupulumutsa.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/091.mp3
150
91