Buku Loyera
|
| 1 |
| Munthu amene amakhala m'linga la Wopambanazonse, iye amene amakhala mumthunzi mwa Mphambe, |
| 2 |
| adzanena kwa Chauta kuti, “Inu ndinu kothaŵira kwanga ndi linga langa, ndinu Mulungu wanga amene ndimakukhulupirirani.” |
| 3 |
| Ndithu, Iye adzakupulumutsa ku msampha wa wosaka, ndiponso ku mliri woopsa. |
| 4 |
| Adzakuphimba ndi nthenga za mapiko ake, udzapeza malo othaŵirako m'mapikomo. Kukhulupirika kwake kumateteza monga chishango ndi lihawo. |
| 5 |
| Sudzachita mantha ndi zoopsa zausiku, kapena nkhondo nthaŵi yamasana. |
| 6 |
| Sudzaopanso mliri wogwa usiku, kapena zoononga moyo masana. |
| 7 |
| Anzako chikwi chimodzi angathe kuphedwa pambali pakopa, kapena zikwi khumi ku dzanja lako lamanja, koma iwe zoopsazo sizidzakukhudza. |
| 8 |
| Uzingopenya ndi maso ako, ndipo udzaona m'mene amalangidwira anthu ochita zoipa. |
| 9 |
| Chifukwa chakuti wavomera Chauta kuti akhale malo ako othaŵirako, wavomera Wopambanazonse kuti akhale malo ako okhalamo, |
| 10 |
| zoipa sizidzakugwera, zoopsa sizidzafika pafupi ndi nyumba yako. |
| 11 |
| Chauta adzapatsa angelo ake ntchito yoti azikulonda kulikonse kumene upite. |
| 12 |
| Adzakunyamula m'manja mwao, kuwopa kuti phazi lako lingapweteke ndi mwala. |
| 13 |
| Udzatha kuponda mkango ndi njoka, zoonadi udzaponda ndi phazi lako msona wa mkango ndiponso chinjoka. |
| 14 |
| Pakuti amene amandikangamira Ine Mulungu mwachikondi, ndidzampulumutsa. Ndidzamteteza popeza kuti amadziŵa dzina langa. |
| 15 |
| Akadzandiitana, ndidzamuyankha, ndidzakhala naye pa nthaŵi yamavuto. Ndidzamlanditsa ndi kumlemekeza. |
| 16 |
| Ndidzampatsa moyo wautali ndi kumpulumutsa. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/091.mp3
150
91