Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo. Nyimbo ya pa tsiku la Sabata. Nʼkwabwino kutamanda Yehova ndi kuyimbira nyimbo dzina lanu, Inu Wammwambamwamba, |
| 2 |
| Kulengeza chikondi chanu mmawa, ndi kukhulupirika kwanu nthawi ya usiku, |
| 3 |
| kuyimbira nyimbo choyimbira cha zingwe khumi ndi mayimbidwe abwino a zeze. |
| 4 |
| Pakuti Inu mumandisangalatsa ndi ntchito zanu, Inu Yehova; Ine ndikuyimba mwachimwemwe pa ntchito ya manja anu. |
| 5 |
| Ndi yayikuludi ntchito yanu Yehova, maganizo anu ndi ozamadi! |
| 6 |
| Munthu wopanda nzeru sadziwa, zitsiru sizizindikira, |
| 7 |
| kuti ngakhale anthu oyipa aphuka ngati udzu ndipo anthu onse ochita zoyipa apindula, adzawonongedwa kwamuyaya. |
| 8 |
| Koma Inu Yehova, ndinu wokwezedwa kwamuyaya. |
| 9 |
| Zoonadi adani anu Yehova, zoonadi adani anu adzawonongeka; onse ochita zoyipa adzabalalitsidwa. |
| 10 |
| Inu mwakweza nyanga yanga ngati nyanga ya njati; mafuta abwino akhuthulidwa pamutu wanga. |
| 11 |
| Maso anga aona kugonjetsedwa kwa olimbana nane, makutu anga amva za kugwa kwa amaliwongo anga oyipa. |
| 12 |
| Anthu olungama adzaphuka ngati mtengo wa mgwalangwa, adzakula ngati mkungudza wa ku Lebanoni; |
| 13 |
| odzalidwa mʼnyumba ya Yehova, adzakula bwino mʼmabwalo a Mulungu wathu. |
| 14 |
| Iwo adzaberekabe zipatso mu ukalamba wawo, adzakhala anthete ndi obiriwira, |
| 15 |
| kulengeza kuti, “Yehova ndi wolungama; Iye ndiye Thanthwe langa, ndipo mwa Iye mulibe choyipa.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/092.mp3
150
92