Buku Loyera
|
| 1 |
| Nkwabwino kuthokoza Chauta, kuimba nyimbo zotamanda dzina lanu, Inu Wopambanazonse. |
| 2 |
| Nkwabwino m'maŵa kulalika za chikondi chanu chosasinthika, ndipo usiku kusimba za kukhulupirika kwanu, |
| 3 |
| poimba nyimbo zokoma ndi gitara, zeze ndi pangwe. |
| 4 |
| Inu Chauta, mwandisangalatsa ndi ntchito zanu. Motero ndikufuula ndi chimwemwe chifukwa cha zimene Inu mwachita. |
| 5 |
| Ntchito zanu si kukula kwake, Inu Chauta! Maganizo anu si kuzama kwake! |
| 6 |
| Munthu wopanda nzeru sangadziŵe, munthu wopusa sangamvetse zimenezi, zakuti, |
| 7 |
| ngakhale anthu oipa aziphuka ngati udzu, ndipo anthu ochimwa zinthu ziziŵayendera bwino, kwao nkuwonongeka kwamuyaya. |
| 8 |
| Inu nokha Chauta, ndinu Wopambanazonse mpaka muyaya. |
| 9 |
| Ndithudi adani anu, Inu Chauta, adani anu adzaonongeka, onse ochita zoipa adzamwazikana. |
| 10 |
| Koma ine mwandilimbitsa ngati njati. Mwandidzoza ndi mafuta atsopano. |
| 11 |
| Maso anga aona kuwonongeka kwa adani anga, makutu anga amva za kugwa kwa adani ondiwukira. |
| 12 |
| Anthu okondweretsa Mulungu zinthu zimaŵayendera bwino ngati mitengo ya mgwalangwa, amakula ngati mikungudza ya ku Lebanoni. |
| 13 |
| Ali ngati mitengo yookedwa m'Nyumba ya Chauta, yokondwa m'mabwalo a Nyumba ya Mulungu wathu. |
| 14 |
| Mitengoyi imabalabe zipatso ngakhale itakalamba, nthaŵi zonse imakhala ndi madzi ndipo imabiriŵira, |
| 15 |
| imaonetsa kuti Chauta ndi wolungama. Iye ndiye thanthwe langa mwa Iye mulibe chokhota. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/092.mp3
150
92