×

Buku Lopatulika 1992

MASALIMO 93

1
Yehova acita ufumu; wadzibveka ndi ukulu; Wadzibveka Yehova, wadzimangirira mphamvu m'cuuno; Dziko lomwe lokhalamo anthu likhazikika, silidzagwedezeka.
2
Mpando wacifumu wanu ukhazikika kuyambira kale lija; Inu ndinu wosayambira ndi kale, lomwe.
3
Mitsinje ikweza, Yehova, Mitsinje ikweza mkokomo wao; Mitsinje ikweza mafunde ao.
4
Yehova Wam'mwamba ndiye wamphamvu, Wakuposa mkokomo wa madzi ambiri, Ndi mafunde olimba a nyanja.
5
Mboni zanu zibvomerezeka ndithu; Ciyero ciyenera nyumba yanu, Yehova, ku nthawi za muyaya.
Chewa Bible 1992
Zambia Bible Society, Malawi Bible Society and Zimbabwe Bible Society
:
Sungani Zolemba