|
| 1 |
|
| Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango, Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu. |
|
| 2 |
|
| Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi; bwezerani kwa odzikuza zowayenera. |
|
| 3 |
|
| Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova, mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe? |
|
| 4 |
|
| Amakhuthula mawu onyada; onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza. |
|
| 5 |
|
| Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova; amapondereza cholowa chanu. |
|
| 6 |
|
| Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko; amapha ana amasiye. |
|
| 7 |
|
| Iwo amati, “Yehova sakuona; Mulungu wa Yakobo salabadirako.” |
|
| 8 |
|
| Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu; zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru? |
|
| 9 |
|
| Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva? Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona? |
|
| 10 |
|
| Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga? Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru? |
|
| 11 |
|
| Yehova amadziwa maganizo a munthu; Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe. |
|
| 12 |
|
| Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza, munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu; |
|
| 13 |
|
| mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto, mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje. |
|
| 14 |
|
| Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake; Iye sadzasiya cholowa chake. |
|
| 15 |
|
| Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo, ndipo onse olungama mtima adzachitsata. |
|
| 16 |
|
| Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa? Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa? |
|
| 17 |
|
| Yehova akanapanda kundithandiza, bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa. |
|
| 18 |
|
| Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,” chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza. |
|
| 19 |
|
| Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga, chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga. |
|
| 20 |
|
| Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake? |
|
| 21 |
|
| Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe. |
|
| 22 |
|
| Koma Yehova wakhala linga langa, ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako. |
|
| 23 |
|
| Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo; Yehova Mulungu wathu adzawawononga. |
|
|
|
|