Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe, tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu |
| 2 |
| Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo. |
| 3 |
| Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu, mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse. |
| 4 |
| Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi, ndipo msonga za mapiri ndi zake. |
| 5 |
| Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye, ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma. |
| 6 |
| Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira, tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu; |
| 7 |
| pakuti Iye ndiye Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za mʼdzanja lake. Lero ngati inu mumva mawu ake, |
| 8 |
| musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba, monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu. |
| 9 |
| Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa, ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita. |
| 10 |
| Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo; ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera ndipo sanadziwe njira zanga.” |
| 11 |
| Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti, “Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.” |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/095.mp3
150
95