Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale; magombe akutali akondwere. |
| 2 |
| Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira; chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu. |
| 3 |
| Moto umapita patsogolo pake ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse. |
| 4 |
| Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse; dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera. |
| 5 |
| Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova, pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi. |
| 6 |
| Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake, ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake. |
| 7 |
| Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi, iwo amene amanyadira mafano; mulambireni, inu milungu yonse! |
| 8 |
| Ziyoni akumva ndipo akukondwera, midzi ya Yuda ikusangalala chifukwa cha maweruzo anu Yehova. |
| 9 |
| Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi; ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse. |
| 10 |
| Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa |
| 11 |
| Kuwala kumafika pa anthu olungama, ndi chimwemwe kwa olungama mtima. |
| 12 |
| Kondwerani mwa Yehova Inu olungama ndipo tamandani dzina lake loyera. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/097.mp3
150
97