Buku Loyera
|
| 1 |
| Chauta ndiye Mfumu, anthu a pa dziko lapansi akondwere, anthu onse a m'mbali mwa nyanja asangalale. |
| 2 |
| Mitambo ndi mdima waukulu zamzinga Chauta. Amalamulira molungama, mu ufumu wake mulibe tsankho. |
| 3 |
| Moto umapita patsogolo pake, umapsereza adani ake omzinga kulikonse. |
| 4 |
| Zing'aning'ani zake zimaŵalitsa dziko lonse lapansi, dziko lonse limapenya nkugwedezeka. |
| 5 |
| Mapiri amasungunuka ngati sera pamaso pa Chauta, ndiye wolamulira dziko lonse lapansi. |
| 6 |
| Zakumwamba zimalalika za kulungama kwake, ndipo anthu a mitundu yonse amaona ulemerero wake. |
| 7 |
| Onse opembedza milungu yonama, amene amanyadira mafano achabechabe, amachititsidwa manyazi, pakuti milungu ina yonse imagonjera Chauta. |
| 8 |
| Anthu a ku Ziyoni akumva, ndipo akusangalala, midzi ya ku Yuda nayonso ikukondwera chifukwa cha kaweruzidwe kanu, Inu Chauta. |
| 9 |
| Pakuti Inu Chauta ndinu Wopambanazonse, wolamulira dziko lonse lapansi. Ndinu amphamvu kupambana milungu yonse. |
| 10 |
| Chauta amakonda anthu odana ndi zoipa. Iye amasunga moyo wa anthu ake oyera mtima. Amaŵapulumutsa kwa anthu oipa. |
| 11 |
| Amaŵalira anthu amene amamumvera, ndipo anthuwo amakhaladi ndi chimwemwe. |
| 12 |
| Inu ndi anthu a Chauta, kondwerani mwa iye, ndipo mumthokoze potchula dzina lake loyera. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewablydc/psalms/097.mp3
150
97