Mawu a Mulungu 2016
|
| 1 |
| Salimo. Imbirani Yehova nyimbo yatsopano, pakuti Iyeyo wachita zinthu zodabwitsa; dzanja lake lamanja ndi mkono wake woyera zamuchitira chipulumutso. |
| 2 |
| Yehova waonetsa chipulumutso chake ndipo waulula chilungamo chake kwa anthu a mitundu ina. |
| 3 |
| Iye wakumbukira chikondi chake ndi kukhulupirika kwake pa Aisraeli; malekezero onse a dziko lapansi aona chipulumutso cha Mulungu wathu. |
| 4 |
| Fuwulani mwachimwemwe kwa Yehova, dziko lonse lapansi, muyimbireni nyimbo mofuwula ndi mokondwera. |
| 5 |
| Imbirani Yehova nyimbo ndi zeze, ndi zeze ndi mawu a kuyimba, |
| 6 |
| ndi malipenga ndi kuliza kwa nyanga ya nkhosa yayimuna fuwulani mwachimwemwe pamaso pa Yehova Mfumu. |
| 7 |
| Nyanja ikokome pamodzi ndi zonse zili mʼmenemo, dziko lonse ndi onse amene amakhala mʼmenemo. |
| 8 |
| Mitsinje iwombe mʼmanja mwawo, mapiri ayimbe pamodzi mwachimwemwe; |
| 9 |
| izo ziyimbe pamaso pa Yehova, pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi. Adzaweruza dziko lonse mwachilungamo, ndi mitundu ya anthu mosakondera. |
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa2016/psalms/098.mp3
150
98