Ndipo akerubi afunyululire mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zipenyane; nkhope za akerubi zipenye kuchotetezerapo.
Ndipo pomwepo ndidzakomana ndi iwe, ndi kulankhula ndi iwe, ndili pamwamba pa chotetezerapo, pakati pa akerubi awiriwo okhala pa likasa la mboni, zonse zimene ndidzakuuza za ana a Israele.
Ndipo uzipanga choikapo nyali cha golide woona; choikapocho chisulidwe mapangidwe ake, tsinde lake ndi thupi lake; zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zikhale zochokera m'mwemo;
ndipo m'mbali zake mutuluke mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m'mbali yake ina, ndi mphanda zitatu za choikapo nyalicho zituluke m'mbali inzake.
Ku mphanda ina kukhale zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi ku mphanda inzake zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; zitere mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho.
pakhale mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri zotuluka m'mwemo; itere ku mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyalicho.