Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo akuyandikire Aroni mbale wako, ndi ana ace amuna pamodzi naye, mwa ana a Israyeli, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe, ndiwo Aroni, Nadabu, ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara, ana a Aroni. |
| 2 |
| Ndipo usokere Aroni mbale wako zobvala zopatulika, zikhale zaulemerero ndi zokoma. |
| 3 |
| Ndipou lankhule ndi onse a mtima waluso, amene ndawadzaza ndi mzimu waluso, kuti amsokere Aroni zobvala apatulidwe nazo, andicitire Ine nchito ya nsembe. |
| 4 |
| Ndipo zobvala azisoka ndizi: capacifuwa ndi efodi, ndi mwinjiro, ndi malaya opikapika, ndi nduwira, ndi mpango; tero apangire Aroni mbale wako ndi ana ace zobvala zopatulika, kuti andicitire Ine nchito ya nsembe, |
| 5 |
| Ndipo atenge golidi, ndi lamadzi ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. |
| 6 |
| Naombe efodi ndi golidi, ndi lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira ndi bafuta wa thonje losansitsa, nchito ya mmisiri. |
| 7 |
| Akhale nazo zapamapewa ziwiri zomangika ku nsonga zace ziwiri, kuti amangike nazo. |
| 8 |
| Ndipo mpango wa efodi, wokhala pamenepo, kuti ammange nao, ukhale wa ciombedwe comweco, ndi woombera kumodzi, wagolidi, ndi thonje lamadzi, ndi lofiirira ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. |
| 9 |
| Ndipo utenge miyala iwiri yaberulo, nulocepo maina a ana a Israyeli; |
| 10 |
| maina asanu ndi limodzi pa mwala wina, ndi maina asanu ndi limodzi otsala pa mwala unzace, mwa kubadwa kwao. |
| 11 |
| Uloce miyala iwiriyo ndi maina a ana a Israyeli, monga mwa nchito ya woloca miyala, monga malembedwe a cosindikizira, uipange igwirike ndi zoikamo zagolidi, |
| 12 |
| Ndipo ulike miyala iwiriyo pa zapamapewa za efodi, ikhale miyala ya cikumbutso ca ana a Israyeli; ndipo Aroni azinyamula maina ao pa mapewa ace awiri, akhale cikumbutso pamaso pa Yehova. |
| 13 |
| Ndipo upange zoikamo za golidi; |
| 14 |
| ndi maunyolo awiri a golidi woona; uwapote ngati zingwe, nchito yopota; numange maunyolo opotawo pazoikamo. |
| 15 |
| Upangenso capacifuwa ca ciweruzo, nchito ya mmisiri; uciombe mwa ciombedwe ca efodi; uciombe ndi golidi, lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiira, ndi bafuta wa thonje losansitsa. |
| 16 |
| Cikhale campwamphwa, copindika, utali wace cikhato cimodzi, ndi kupingasa kwace cikhato cimodzi. |
| 17 |
| Ndipo uikepo miyala yoikikapo, mizere inai ya miyala; mzere wa odemu, pitida, ndi bareketi, ndiyo ya mzere woyamba; |
| 18 |
| ndi mzere waciwiri wa nofeki, safiri, ndi yahaloni; |
| 19 |
| ndi mizere wacitatu wa lesemu, sibu, ndi akalama; |
| 20 |
| ndi mzere wacinai wa tarisisi, sohamu, ndi yasefe; zikhale zogwirika ndi golidi m'zoikamo zao. |
| 21 |
| Ndi miyalayi ikhale monga mwa maina a ana a Israyeli, khumindiawiri, monga maina ao; monga malocedwe a cosindikizira, yonse ikhale monga maina ao, kwa mafuko khumi ndi awiri. |
| 22 |
| Upangenso maunyolo pa capacifuwa ngati zingwe, nchito yopota, ya golidi woona. |
| 23 |
| Nupangire pa capacifuwa mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzika mphete ziwirizo pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa. |
| 24 |
| Numange maunyolo awiri opota agolidi ku mphete ziwiri pansonga pace pa capacifuwa. |
| 25 |
| Koma nsonga zace ziwiri za maunyolo opotawo uzimange ku zoikamo ziwiri, ndi kuziika pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'tsogolo mwace. |
| 26 |
| Ndipo upange mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa nsonga zace ziwiri za capacifuwa, m'mphepete mwace, m katimo ku mbali ya kuefodi. |
| 27 |
| Upangenso mphete ziwiri zagolidi, ndi kuzimanga pa zapamapewa ziwiri za efodi, m'munsi, ku mbali yace ya kutsogolo, pafupi pa msoko wace, pamwamba pa mpango wa efodi. |
| 28 |
| Ndipo amange capacifuwa pa mphete zace ndi mphete za efodi ndi mkuzi wamadzi, kuti cikhale pa mpango wa efodi; ndi kuti capacifuwa cisamasuke paefodi, |
| 29 |
| Ndipo Aroni azinyamula maina a ana a Israyeli pa capacifuwa ca ciweruzo pamtima pace, pakulowa iye m'malo opatulika, akhale cikumbutso pankhope pa Yehova kosalekeza. |
| 30 |
| Ndipo uike Urimu ndi Tumimu mwa capacifuwa ca ciweruzo; ndipo zikhale pa mtima wa Aroni, pakulowa iye pamaso pa Yehova; ndipo Aroni azinyamula ciweruzo ca ana a Israyeli pamtima pace pamaso pa Yehova kosalekeza. |
| 31 |
| Ndipo uombe mwinjiro wa efodi ndi lamadzi lokha. |
| 32 |
| Ndipo polowa mutu pakhale pakati pace; pakhale mkawo pozungulira polowa pace, wa nchito yoomba, ngati polowa pa malaya ociniiriza, pangang'ambike. |
| 33 |
| Ndipo pa mbinyiru wace upange makangaza a lamadzi, ndi lofiirira, ndi lofiirira, pambinyiru pace pozungulira, ndi kuwapakiza ndi miliu yagolidi pozungulira; |
| 34 |
| mliu wagolidi ndi khangaza, mliu wagolidi ndi khangaza, pa mbinyiru wa mwinjiro pozungulira. |
| 35 |
| Ndipo Aroni aubvale kuti atumikire nao; ndipo limveke liu lace pakulowa iye m'malo opatulika pamaso pa Yehova, ndi pakuturuka iye, kuti asafe. |
| 36 |
| Ndipo upange golidi waphanthiphanthi woona, ndi kulocapo, monga malocedwe a cosindikizira. KUPATULIKIRA YEHOVA. |
| 37 |
| Nuciike pamkuzi wamadzi, ndipo cikhale panduwira, cikhale patsogolo pace pa nduwira. |
| 38 |
| Ndipo cizikhala pamphumi pace pa Aroni, ndipo Aroni azinyamula mphulupulu ya zopatulidwa, zimene ana a Israyeli azipatulira, ndi zopereka zao zonse zopatulira; ndipo cizikhala pamphumi pace kosalekeza, kuti alandiridwe pamaso pa Yehova. |
| 39 |
| Ndipo upikule maraya am'kati abafuta a thonje losansitsa, nusoke nduwira wabafuta, nusokenso mpango wopikapika. |
| 40 |
| Ndipo usokere ana a Aroni maraya am'kati, nuwasokere mipango; uwasokerenso akapa akhale aulemerero ndi okoma. |
| 41 |
| Ndipo ubveke nazo Aroni mbale wako, ndi ana ace omwe; ndi a kuwadzoza, ndi kudzaza dzanja lao, ndi kuwapatula, andicitire Ine nchito ya nsembe. |
| 42 |
| Uwasokerenso zobvala za miyendo za bafuta wa thome losansitsa kubisa marisece ao; ziyambire m'cuuno zifikire kuncafu. |
| 43 |
| Ndipo azibvale Aroni, ndi ana ace, pakulowa iwo ku cihema cokomanako, kapena poyandikiza iwo ku guwa la nsembe kutumikira m'malo opatulika; anganyamule mphulupulu, nangafe; likhale lemba losatha la iye ndi mbumba zace pambuyo pace. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/exodus/028.mp3
40
28