Ndipo Bezalele anapanga likasa la mtengo wakasiya; utali wake mikono iwiri ndi hafu, ndi kupingasa kwake mkono ndi hafu, ndi msinkhu wake mkono ndi hafu;
Ndipo akerubi anafunyulira mapiko ao m'mwamba, ndi kuphimba chotetezerapo ndi mapiko ao, ndi nkhope zao zopenyana; zinapenya kuchotetezerapo nkhope zao.
Ndipo anapanga choikapo nyali cha golide woona; mapangidwe ake a choikapo nyalicho anachita chosula, tsinde lake ndi thupi lake, zikho zake, mitu yake, ndi maluwa ake zinakhala zochokera m'mwemo;
ndi m'mbali zake munatuluka mphanda zisanu ndi imodzi; mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake imodzi, ndi mphanda zitatu za choikapo nyali zotuluka m'mbali yake ina;
pa mphanda imodzi panali zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa; ndi pa mphanda ina zikho zitatu zopangika ngati katungurume, mutu ndi luwa zinatero mphanda zisanu ndi imodzi zotuluka m'choikapo nyali.
ndipo panali mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, ndi mutu pansi pa mphanda ziwiri, zotuluka m'mwemo, inatero pa mphanda zisanu ndi imodzi zochokera m'mwemo.
Ndipo anapanga guwa la nsembe lofukizapo la mtengo wakasiya; utali wake mkono, ndi kupingasa kwake mkono, laphwamphwa; ndi msinkhu wake mikono iwiri; nyanga zake zinatuluka m'mwemo.
Ndipo analipangira mphete ziwiri zagolide pansi pa mkombero wake, pangodya zake ziwiri, pa mbali zake ziwiri, zikhale zopisamo mphiko kulinyamulira nazo.