Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, |
| 2 |
| Tsiku loyamba la mwezi woyamba ukautse kacisi wa cihema cokomanako. |
| 3 |
| Ndipo ukaikemo likasa la mboni, nucinge likasalo ndi nsaru yocingayo. |
| 4 |
| Ulongenso gomelo, nukonzerepo zokonzera zace; ulongenso coikapo nyalico, ndi kuyatsa nyali zace. |
| 5 |
| Ndipo ukaike guwa la nsembe lofukizapo lazolidi cakuno ca likasa la mboni, numange pakacisi nsaru yotsekera pakhomo. |
| 6 |
| Ndipo ukaike guwa la nsembe yopsereza kunja kwa khomo la kacisi wa cihema cokomanako. |
| 7 |
| Ukaikenso mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe, ndi kuthiramo madzi. |
| 8 |
| Ndipo ukamange mpandawo pozungulira, ndi kupacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo. |
| 9 |
| Pamenepo ukatenge mafuta odzoza, ndi kudzoza nao kacisi, ndi zonse ziri m'mwemo, ndi kumpatula, ndi zipangizo zace zonse; ndipo adzakhala wopatulika. |
| 10 |
| Ndipo udzoze guwa la nsembe yopsereza, ndi zipangizo zace zonse, ndi kulipatula guwalo; ndipo guwalo lidzakhala lopatulikitsa. |
| 11 |
| Udzozenso mkhate ndi tsinde lace, ndi kuupatula. |
| 12 |
| Ndipo ubwere nao Aroni ndi ana ace amuna ku khomo la cihema cokomanako, ndi kuwasambitsa ndi madzi. |
| 13 |
| Nubveke Aroni cobvala zopatulikazo; ndi kumdzoza, ndi kumpatwa andicitire Ine nchito ya nsembe. |
| 14 |
| Ndipo ubwere nao ana ace amuna ndi kuwabveka maraya am'kati; |
| 15 |
| nuwadzoze, monga unadzoza atate wao, kuti andicitire nchito ya nsembe; ndi kudzozedwa kwao kuwakhalire unsembe wosatha mwa mibadwo yao. |
| 16 |
| Anatero Mose; monga mwa zonse Yehova adamuuza, momwemo anacita. |
| 17 |
| Ndipo kunali, mwezi woyamba wa caka caciwiri, tsiku loyamba la mwezi, anautsa kacisi. |
| 18 |
| Ndipo Mose anautsa kacisi, nakhazika makamwa ace, naimika matabwa ace, namangapo mitanda yace, nautsa mizati ndi nsanamira zace. |
| 19 |
| Ndipo anayalika hema pamwamba pa kacisi, naika cophimba ca cihema pamwamba pace; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 20 |
| Ndipo anatenga mboniyo, naiika mlikasa, napisa mphiko palikasa, naika cotetezerapo pamwamba pa likasa; |
| 21 |
| nalowa nalo likasa m'kacisi, napacika nsaru yocinga, nacinga likasa la mboni; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 22 |
| Ndipo anaika gomelo m'cihema cokomanako, pa mbali ya kumpoto ya kacisi, kunja kwa nsaru yocinga. |
| 23 |
| Nakonzerapo mkate pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 24 |
| Ndipo anaika coikapo nyali m'cihema cokomanako, popenyana ndi gome, pa mbali ya kumwela ya kacisi. |
| 25 |
| Nayatsa nyalizo pamaso pa Yehova; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 26 |
| Ndipo anaika guwa la nsembe lagolidi m'cihema cokomanako cakuno ca nsaru yocinga; |
| 27 |
| nafukizapo cofukiza ca pfungo lokoma; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 28 |
| Ndipo anapacika kukacisi nsaru yotsekera pakhomo. |
| 29 |
| Ndipo anaika guwa la nsembe yopsereza pa khomo la kacisi wa cihema cokomanako, natenthapo nsembe yopsereza, ndi nsembe yaufa; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 30 |
| Ndipo anaika mkhate pakati pa cihema cokomanako, ndi guwa la nsembe; nathiramo madzi osamba. |
| 31 |
| Ndipo Mose ndi Aroni ndi ana ace amuna anasamba manja ao ndi mapazi ao m'menemo; |
| 32 |
| pakulowa iwo m'cihema cokomanako, ndi pakuyandikiza guwa la nsembe anasamba; monga Yehova adamuuza Mose. |
| 33 |
| Ndipo anautsa mpanda pozungulira pa cihema ndi guwa la nsembe, napacika nsaru yotsekera pa cipata ca pabwalo. Momwemo Mose anatsiriza nchitoyi. |
| 34 |
| Pamenepo mtambo unaphimba cihema cokomanako, ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisiyo. |
| 35 |
| Ndipo Mose sanathe kulowa m'cihema cokomanako, popeza mtambo unakhalabe pamenepo; ndi ulemerero wa Yehova unadzaza kacisi. |
| 36 |
| Ndipo pakukwera mtambo kucokera kukacisi, ana a Israyeli amayenda maulendo ao onse; |
| 37 |
| koma ukapanda kukwera mtambo, samayenda ulendo wao kufikira tsiku loti wakwera. |
| 38 |
| Pakuti mtambo wa Yehova unakhala pakacisi msana, ndi usiku munali moto m'menemo, pamaso pa mbumba yonse ya Israyeli, m'maulendo ao onse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/exodus/040.mp3
40
40