Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo pambuyo pace Mose ndi Aroni analowa nanena ndi Farao, Atero Yehova, Mulungu wa Israyeli, Lola anthu anga apite, kundicitira madyerero m'cipululu. |
| 2 |
| Koma Farao anati, Yehova ndani, kuti ndimvere mau ace ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziwa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite. |
| 3 |
| Ndipo iwo anati, Mulungu wa Ahebri wakomana ndi ife; timuketu ulendo wa masiku atatu m'cipululu, kumphera nsembe Yehova Mulungu wathu; kuti angatikumike ndi mliri, kapena ndi lupanga, |
| 4 |
| Ndipo mfumu ya Aigupto inanena nao, Inu, Mose ndi Aroni, cifukwa ninji mumasulira anthu nchito zao? Mukani ku akatundu anu. |
| 5 |
| Farao anatinso, Taonani, anthu a m'dziko ndiwo ambiri tsopano; ndipo inu muwapumitsa ku akatundu ao, |
| 6 |
| Ndipo tsiku lomwelo Farao analamulira akufulumiza anthu, ndi akapitao ao, ndi kuti, |
| 7 |
| Musawapatsanso anthu udzu wakupanga nao njerwa monga kale; apite okha adzifunire udzu. |
| 8 |
| Ndipo muziwawerengera njerwa, monga momwe anapanga kale; musacepsapo, popeza acita cilezi; cifukwa cace alikupfuula, ndi kuti, Timuke, timphere nsembe Mulungu wathu. |
| 9 |
| Ilimbike nchito pa amunawo, kuti aigwiritsitse, asasamalire mau amabodza. |
| 10 |
| Ndipo akufulumiza anthu ndi akapitao ao anaturuka, nanena ndi anthu ndi kuti, Atero Farao, Kulibe kukupatsani udzu. |
| 11 |
| Mukani inu nokha, dzifunireni udzu komwe muupeza; pakuti palibe kanthu kadzacepa pa nchito yanu. |
| 12 |
| Pamenepo anthuwo anabalalika m'dziko lonse la Aigupto kufuna ciputu ngati udzu. |
| 13 |
| Ndipo akufulumiza anawakakamiza, ndi kuti, Tsirizani nchito zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace, monga muja munali ndi udzu. |
| 14 |
| Ndipo anapanda akapitao a ana a Israyeli, amene ofulumiza a Farao adawaika, ndi kuti, Nanga dzulo ndi lero simunatsiriza bwanji nchito yanu yoneneka ya njerwa, monga kale? |
| 15 |
| Pamenepo akapitao a ana a Israyeli anafika nalirira Farao, nati, Mwatero bwanji ndi akapolo anu? |
| 16 |
| Udzu osawapatsa akapolo anu, ndipo amanena ndi ife, Umbani njerwa; ndipo, taonani, amapanda akapolo anu; koma kulakwa nkwa anthu anu. |
| 17 |
| Koma iye anati, Aulesi inu, aulesi: cifukwa cace mulikunena, Timuke, timphere nsembe Yehova. |
| 18 |
| Mukani tsopano, gwirani nchito; pakuti sadzakupatsani udzu, koma muonetse ciwerengero cace ca njerwa. |
| 19 |
| Ndipo akapitao a ana a Israyeli anaona kuti kudawaipira, pamene ananena, Musamacepetsa njerwa zanu, nchito ya tsiku pa tsiku lace. |
| 20 |
| Ndipo poturuka kwa Farao iwo anakomana ndi Mose ndi Aroni, alikuima popenyana nao; |
| 21 |
| ndipo ananena nao, Yehova akupenyeni, naweruze; pakuti mwatinyansitsa pamaso pa Farao, ndi pamaso pa anyamata ace, ndi kuwapatsa lupanga m'dzanja lao kutipha nalo. |
| 22 |
| Pamenepo Mose anabwerera namka kwa Yehova, nati, Ambuye, mwawacitiranji coipa anthuwa? mwandituma bwanji? |
| 23 |
| Popeza kuyambira kuja ndinafika kwa Farao kulankhula m'dzina lanu, anawacitira coipa anthuwa; ndipo simunalanditsa anthu anu konse. |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/exodus/005.mp3
40
5