Buku Lopatulika 1992
|
| 1 |
| Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona comwe ndidzacitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lace. |
| 2 |
| Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOV A: |
| 3 |
| ndipo ndinaonekera Abrahamu, Isake ndi Yakobo, Mulungu Wamphamvuyonse; koma sindinadziwika kwa iwo ndi dzina langa YEHOV A. |
| 4 |
| Ndipo ndinakhazikitsanso nao cipangano canga, kuwapatsa dziko la Kanani, dziko la maulendo ao, anali alendo m'mwemo. |
| 5 |
| Ndamvanso kubuula kwa ana a Israyeli, amene Aaigupto awayesa akapolo; ndipo ndakumbukila cipangano canga. |
| 6 |
| Cifukwa cace nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakuturutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo akuru; |
| 7 |
| ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakuturutsa inu pansi pa akatundu a Aaigupto. |
| 8 |
| Ndipo ndidzakulowetsani m'dziko limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova. |
| 9 |
| Ndipo Mose ananena comweco ndi ana a Israyeli; koma sanamvera Mose cifukwa ca kuwawa mtima, ndi ukapolo wolemera. |
| 10 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, |
| 11 |
| Lowa, lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto, kuti alole ana a Israyeli aturuke m'dziko lace. |
| 12 |
| Koma Mose ananena pamaso pa Mulungu, ndi kuti, Onani, ana a Israyeli sanandimvera ine; adzandimvera bwanji Farao, ndine wa milomo yosadula? |
| 13 |
| Ndipo Yehova ananena ndi Mose ndi Aroni, nawalangiza za ana a Israyeli, ndi za Farao mfumu ya Aigupto, kuti aturutse ana a Israyeli m'dziko la Aigupto. |
| 14 |
| Akuru a mbumba za makolo ao ndi awa: ana amuna a Rubeni, woyamba wa Israyeli ndiwo: Hanoki ndi Palu, Hezroni, ndi Karmi; amene ndiwo mabanja a Rubeni. |
| 15 |
| Ndi ana amuna a Simeoni ndiwo: Yemweli, ndi Yamini, ndi Ohadi, Yakini, ndi Zohari, ndi Sauli mwana wa mkazi wa m'Kanani; amene ndiwo mabanja a Simeoni. |
| 16 |
| Ndipo maina a ana amuna a Levi, mwa kubadwa kwao ndiwo: Gerisoni, ndi Kohati, ndi Merari; ndipo zaka za moyo wa Levi ndizo zana limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. |
| 17 |
| Ana amuna a Gerisoni ndiwo: Libni ndi Simei, mwa mabanja ao. |
| 18 |
| Ndi ana amuna a Kohati ndiwo: Amramu ndi Izara, ndi Hebroni, ndi Uziyeli; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu kudza zitatu. |
| 19 |
| Ndipo ana amuna a Merai ndiwo: Mali ndi Musi. Amenewo ndiwo mabanja a Levi mwa kubadwa kwao. |
| 20 |
| Ndipo Amramu anadzitengera Yokobedi mlongo wa atate wace akhale mkazi wace; ndipo anambalira Aroni ndi Mose; ndi zaka za moyo wa Amramu ndizo zaria limodzi mphambu makumi atatu kudza zisanu ndi ziwiri. |
| 21 |
| Ndi ana amuna a lzara ndiwo: Kora: ndi Nefegi, ndi Zikiri. |
| 22 |
| Ndi ana amuna a Uziyeli ndiwo: Misayeli, ndi Elisafana, ndi Sitiri. |
| 23 |
| Ndipo Aroni anadzitengera Eliseba, mwana wamkazi wa Aminadabu, mlongo wace wa Nasoni, akhale mkazi wace; ndipo anambalira Nadabu ndi Abihu, Eleazara ndi ltamara. |
| 24 |
| Ndipo ana amuna a Kora ndiwo: Asiri ndi Elikana, ndi Abiasafu; amenewo ndiwo mabanja a Akora. |
| 25 |
| Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana akazi a Putieli akhale mkazi wace, ndipo anambalira Pinehasi. Amenewo ndi akuru a makolo a Alevi mwa mabanja ao. |
| 26 |
| Omwewo ndiwo Aroni ndi Mose amene Yehova ananena nao, Turutsani ana a Israyeli m'dziko la Aigupto mwa makamu ao. |
| 27 |
| Awa ndi omwewo ananena ndi Farao, mfumu ya Aigupto, awaturutse ana a Israyeli m'Aigupto; Mose ndi Aroni amenewa. |
| 28 |
| Ndipo kunali, tsiku limene Yehova ananena ndi Mose m'dziko la Aigupto, |
| 29 |
| Yehova ananena ndi Mose, ndi kuti, Ine ndine Yehova: lankhula ndi Farao mfumu ya Aigupto zonsezi Ine ndizinena nawe. |
| 30 |
| Koma Mose anati pamaso pa Yehova, Onani, ine ndiri wa milome yosadula, ndipo Farao adzandimvera bwanji? |
|
| Sungani Zolemba |
https://beblia.bible:81/BibleAudio/chewa1992/exodus/006.mp3
40
6