×

Buku Loyera

EKSODO 7

1
Chauta adauza Mose kuti, “Taona, ndidzakusandutsa kuti ukhale ngati Mulungu kwa Farao, ndipo mbale wako Aroni ndiye adzakhale ngati mneneri wako.
2
Zonse zimene ndakulamulazi ukazinene, ndipo iye ndiye akauze Farao kuti aŵalole Aisraele kutuluka m'dziko mwake.
3
Komatu ndidzamuumitsa mtima, ndipo ngakhale ndidzachite zozizwitsa zambiri ndi zodabwitsa ku Ejipito,
4
Faraoyo sadzakumverani. Pamenepo ndidzakantha dzikolo, ndipo pochita ntchito zamphamvu, ndidzatsogolera magulu anga, anthu anga Aisraele, kuŵatulutsa ku Ejipito.
5
Apo Aejipito adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta, ndikadzaŵakantha ndi dzanja langa ndi kutulutsa Aisraele m'dziko mwaomo.”
6
Ndipo Mose ndi Aroni adachitadi zomwe Chauta adaŵalamulazo.
7
Pamenepo nkuti Mose ali wa zaka 80 ndipo Aroni wa zaka 83, pa nthaŵi imene ankalankhula ndi Farao.
8
Tsono Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti,
9
“Ngati Farao akulamulani kuti, ‘Chitani chozizwitsa kuti tikukhulupirireni,’ iwe Mose ukauze Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, iponye pansi pamaso pa Farao kuti isanduke njoka.’ ”
10
Choncho Mose ndi Aroni adapita kwa Farao nakachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adaponya pansi ndodo yake ija pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo idasanduka njoka.
11
Zitatero Farao adaitana anthu ake anzeru ndi amatsenga, ndipo iwowo adachitanso zomwezo mwa matsenga ao.
12
Adaponyanso pansi ndodo zao, ndipo zidasanduka njoka. Koma ndodo ya Aroni ija idameza ndodo zaozo.
13
Farao adaumabe mtima, ndipo sadasamale zimene ankamuuzazo monga momwe Chauta adaanenera muja.
14
Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Farao ndi wokanika kwambiri, akukana kulola anthu anga kuti apite.
15
Upite m'maŵa ukakumane naye pamene akupita ku mtsinje wa Nailo. Ukamdikire pambali pa mtsinjewo. Tsono utenge ndodo ija idaasanduka njokayi.
16
Ukamuuze Farao kuti Chauta, Mulungu wa Ahebri, wandituma kwa inu kuti ndikuuzeni mau aŵa: ‘Uŵalole anthu anga apite, akandipembedze ku chipululu. Koma mpaka tsopano lino sudandimverebe.’
17
Zimene Chauta akunena ndi izi, akuti ‘Poona zimene ndichite, udzadziŵa kuti Ine ndinedi Chauta. Taona, ndidzamenya madzi a mu mtsinjewu ndi ndodo ili m'manja mwangayi, ndipo madzi onseŵa adzasanduka magazi.
18
Nsomba zonse zidzafa, ndipo madziwo adzanunkha, kotere kuti Aejipito sadzafunanso kumwa madzi a mu mtsinje umenewu.’ ”
19
Chauta adalamulanso Mose kuti, “Uza Aroni kuti, ‘Tenga ndodo yako, uilozetse ku madzi onse mu Ejipito muno, monga mitsinje, ngalande ndiponso zithaphwi ndi maiŵe omwe. Madziwo adzasanduka magazi, ndipo m'dziko monsemo mudzakhala magazi okhaokha, ngakhale m'zotungira madzi zomwe, zamitengo ndi zamiyala.’ ”
20
Motero Mose ndi Aroni adachita monga momwe Chauta adaŵalamulira. Aroni adasamula ndodo yake namenya madzi amumtsinje pamaso pa Farao ndi nduna zake, ndipo madzi onsewo adasanduka magazi.
21
Nsomba zonse zamumtsinjemo zidafa, ndipo kununkha kwake kwa madziwo kunali kwakuti Aejipito sadathenso kuŵamwa. Ndipo munali magazi okhaokha m'dziko lonse la Ejipito.
22
Tsono amatsenga a ku Ejipito aja nawonso adachita zomwezo mwa matsenga ao, ndipo Farao adakhalabe wokanika. Sadamvere zimene ankanena Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja.
23
Pompo Farao adapotoloka, napita kunyumba kwake osalabadanso zimenezo.
24
Aejipito onse adayamba kukumba m'mbali mwa mtsinje wa Nailo kuti apeze madzi akumwa, chifukwa sankathanso kumwa madzi a mu mtsinjewo.
25
Padapita masiku asanu ndi aŵiri, Chauta ataipitsa mtsinje uja.
Chewa Bible BLYDC
Bible Society of Malawi
:
Sungani Zolemba